The Maravi Post

Switch to desktop Register Login



Mwana wasukulu afa atamwa kolapitsa

BLANTYRE--Apolisi ku Luchenza m'boma la Thyolo achenjeza achinyamata kuti asiye kumwa mowa mwauchidakwa ndi kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza ubongo kuphatikizapo chamba pofuna kuchepetsa ngozi ndi imfa zodza mwadzidzidzi.

Apolisi apereka chenjezoli mnyamata wina wa zaka 21, Shadreck Majanga, wam’mudzi mwa Mgunda m’dera la Sub T/A Nanseta, atapezeka wamwalira posachedwapa atamwa wayini wofululuridwa pamsika wa Luchenza, yomwe amamugulitsa pamtengo wotsika kwambiri kuyerekeza ndi mowa wampaketi wa Chibuku ndi Carlsberg.

Chifukwa cha kutchipa, achinyamata ambiri, kuphatikizapo ana asukulu amakhamukira kumeneko kukamwa wayini uku akusakaniza ndi masacheti kuti alenguke nawo msanga ngati wayiniyo ukuchepera mphamvu.

Tsiku limene Shadreck adamwalira akuti adathawira kusukulu ya Widzo Private School, komwe anali mu Form 4. Anakumana ndi achinyamata anzake ndipo anapapira mowa mpaka madzulo.

Mnyamata wina amene anali ndi malemuyo koma adakana kuti timutchule dzina lake, adati anayamba kumwa cha m’ma 12 koloko mpaka cha m’ma 5 koloko madzulo ndipo mnzakeyo anatitsanzika, nayambapo wakunyumba kwawo. Patatha nthawi pang’ono mpamene anakamva kuti mnzake wafa atagwera m'ngalande.

Iyeyu adati patsikulo anyamatawo adamwa mopyolera muyeso. Mkulu wa apolisi odziwa za kufufuza pa Luchenza Police Station, Inspector Bisalomu, wati apolisi ndi okhudzidwa ndi mmene achinyamata akumwera mowa ndi kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza ubongo
m’tawuni ya Luchenza.

"Nditengerepo mwayi kuti ndichenjeze achinyamata kuti asiyiretu mchitidwe umenewu
ngati akufuna kusunga miyoyo yawo," adatero mkuluyu, n'kuchenjezanso kuti anthu amene amtchayapo chakumwa ayenera kudziwa kuti kumwa mowa wosayezedwa ndi Malawi
Bureau of Standards (MBS) akukunkha imfa.

Achipatala pa Chonde adatsimikiza kuti mnyamatayu adamwalira atavulala m’mutu chifukwa chogwera m’ngalande.

Ulendo wathawo, pamene aphungu a ku Nyumba ya Malamulo adakumana ku likulu la dziko lino ku Lilongwe, potsegulira msonkhano wa Bajeti, Pulezidenti Joyce Banda adaopseza kuti aletsa makampani kufulula ndi kugulitsa mowa wa m'masacheti chifukwa umaononga achinyamata ambiri kaamba koti amauhaukira poti ngotsika mtengo.

Potsiriza pa msonkhanowo, aphungu adagwirizana kuti mtengo wa mowa wa m'masacheti ukwere mtengo pofuna kuti achinyamata, maka ana asukulu mwina angamalephere kugula, koma mpaka pano achinyamatawo akufinyirabe masachetiwo ngati amva kuti dziko likutha mawa.

@2010 The Maravi Post an Eltas EnterPrises INC Publishing Company
Site Developed By JRC

Top Desktop version