Written by JOE CHIBEWA
BLANTRYE--Pamene Atupele Muluzi, mwana wa pulezidenti wakale wa dziko la Malawi Bakili Muluzi, adasankhidwa kukhala wapampando wa chipani cha UDF, kutsimikiza kuti ndiye adzayimire chipanichi pachisankho cha pulezidenti m’chaka cha 2014, funso lidali loti kodi adzapitiriza kukhalabe nduna m’boma la Mayi Joyce Banda?
Panthawiyo, Atupele adayankha kuti alibe maganizo ochoka m’boma ndipo sasiya udindo wake ngati nduna ya boma chifukwa akufuna kuthandiza pa chitukuko cha dziko lino posayang’anira chipani. Koma zinthu zikati zitembenuke munthu sungamvetse ndale za pa Malawi. Lero suyu Atupele watula pansi udindo wake ngati nduna ya Mapulani a Zachuma ndi Chitukuko (Minister of Economic Planning and Development). Nanga chavutanso ndi chiyani?
M’chikalata chomwe walemba pouza nyumba zoulutsa ndi kulemba nkhani (press release), Atupele sadatchule mwamvemvemve chifukwa kapena zifukwa zomwe watulira pansi udindo, koma kwa munthu amene amatsata ndale za m’dziko la Malawi akhoza kudziwa kuti iye ndi wonyansidwa ndiponso wokwiya zedi ndi zomwe atsogoleri a chipani cholamula cha PP adanena pamsonkhano ku Mangochi Loweruka lapitali.
Kumeneko akuti wachiwiri kwa pulezidenti wa dziko lino Khumbo Kachali adanenapo zamwano, zamtopola ndiponso zosakhala bwino kwa pulezidenti wakale Muluzi ndinso kwa Atupele mwini wake. Zitatero, Atupele adalephera kuugwira mtima koma kuchoka m’boma basi. Kunena zoona, ngati m’boma la Mayi Joyce Banda munali nduna imodzi imene anthu ankaitayira kamtengo , anali Atupele chifukwa iye mtima wake adali pokonza zinthu m’dziko lathu posayang’anira chipani.
Adadzipereka kuti ngakhale ali m’chipani cha UDF, adali wokonzeka kugwira ntchito limodzi ndi boma la PP potumikira Amalawi. Koma pakamwa podya mchere apa! A Khumbo sadzamva. Nthawi zina kuayankhula sayankhula bwino pamisonkhano. Mmbuyomu adayankhulanso mwano kwa Amalawi pomwe adati “timayenda m’makomo mwa amanu”? Apa ankaikira kumbuyo Pulezident Joyce Banda pamene Amalawi ndi amabungwe ena ankadzudzula khalidwe la atsogoleri lokonda loyendayenda m’maiko akunja ndi m’dziko mom’muno chifukwa potero akusakaza chuma cha dziko. Anthu adamuukira Khumbo chifukwa cha mawu amtopola amenewo ndipo pambuyo pake adapepesa kwa fuko la Malawi.
Koma wachake ndi wachake. A Khumbo adakalalatanso ku Mangochi, nanena mawu onyoza anzawo, zomwe zapangitsa Atupele kuzitula pansi. Kodi, Amalawi, ndale zotukwanizana tidzasiya liti?
Mmene Joyce Banda adakhala pampando wa upulezidenti wa dziko lino, anthu ambiri, kuphatikizapo ineyo, adali ndi chikhulupiriro kuti zinthu ziyambadi kusintha ku Malawi kuno. Nanji ndi mmene adayambira posankha nduna zina m’boma lake kuchokera m’zipani zotsutsa boma monga UDF ndi Aford!
Anthu adaona mwa Joyce Banda mtsogoleri wofuna kuyanjanitsa Amalawi posayang’anira zipani kapena mtundu. Koma zimene zikukambidwa pano n’zokhumudwitsa zedi. Kodi chiyanjano chija chidanka kuti? Indedi, pakamwa pamapasula.
Ndi mayakhulidwe oterewa atsogoleri anthu sakutithandiza ife Amalawi. Atsogoleri otere alibe mwayi mu 2014. Ulemu ndi wofunika kwa munthu aliyense ndipo, monga akunenera Atupele, tiyeni tipatsane ulemu monga anthu a fuko la Malawi. Tikapanda kutero tidzalephera kumanga dziko lino ndipo mmalo mwake tidzaliphwasula ndi manja anthu omwe.