Written by JOE CHIBEWA
BLANTYRE--Nkhondo yolimbana ndi mliri wa Edzi yakula ndipo pafunika chamuna kuti anthu apambane. Pachifukwa ichi, khonsolo ya Luchenza Municipality m'boma la Thyolo m'chigawo cha kummwera kwa dziko la Malawi yasula anyamata omwe amapalasa njinga zobanduka (za hayala) ndi oyitanira mabasi kuti azikaphunzitsa ndi kufalitsa mauthenga okhudza kapewedwe ka matendawa ndi kufunikira kwa kuyezetsa magazi.
Polankhula ndi achinyamatawo potsegulira maphunziro a masiku asanu masiku apitawa, bwanamkubwa wa khonsoloyi, Gift Rapozo, adati oyitanira mabasi ndi opalasa njinga za hayala ndi ofunikira kwambiri pankhondo yolimbana ndi kufala kwa kachilombo ka HIV m’dziko muno.
Rapozo adati akamachenza ndi makasitomala awo komanso anthu ofuna kukwera mabasi, achinyamatawa atha kumaphunzitsanso anthu za mmene angapewere kachilombo ka HIV kamene kamayambitsa Edzi komanso kufunikira kokayezetsa magazi kuti adziwe mmene alili m’thupi mwawo.
“Nkhondo yolimbana ndi matenda a Edzi si ya munthu mmodzi. Ngati tikufuna kupambana pankhondoyi, aliyense ayenera kutengapo nawo mbali chifukwa aliyense ngofunikira polimbana ndi mliri umenewu,” adatero Rapozo.
Iye adalankhulaponso za kufunika kwa kuthetsa miyambo ina ya makolo athu yomwe ikupititsa patsogolo kufala kwa Edzi ndi matenda ena matenda opatsirana yogonana monga kulowa kufa, kusasa fumbi, fisi, kulowa chokolo ndi miyambo ina.
“Ngati anthu oti mumacheza ndi anthu ambiri patsiku kudzera m’ntchito zanu, muli ndi udindo wophunzitsa anzanu za mmene angapewere kutenga kachilombo ka HIV ndi matenda ena opatsirana kudzera m’kugonana.
“Kudzera muuphungu umene mungapereke kwa makasitomala anu ndi anzanu ocheza nawo, khonsolo ino idzatha kufikira anthu ambiri ndi mauthenga pamatenda a Edzi,” adatero Rapozo.
Gift Nansongole, mmodzi mwa anyamata opalasa njinga za hayala, adati maphunzirowo abwera munthawi yake pamene oyitanira mabasi ndi anjinga akukumana ndi mayesero kuchokera kwa amayi omwe akuti amawakakamiza kuti awatenge koma malipiro ake akangogonana nawo.
“Makasitomala achikazi amatipempha kuti asatipatse ndalama ndipo mmalo mwake tiwawenge chala [tigonane nawo]. Ambiri mwa ife sitimathakupirira ndipo tagonanapo nawo amayi otere,” adaulula chotere Nansongole.
Pafupifupi anthu 20 oyitanira mabasi komanso opalasa njinga za hayala adachita nawo maphunzirowa.
Ndalama zochitira maphunzirowa zidachokera kubungwe la National Aids Committee (NAC) kudzera ku District Implementation Plan (DIP).