The Maravi Post

Switch to desktop Register Login



Dayosizi ya Karonga yayamba kumanga manthu wa tchalichi

MZUZU--Ntchito yomanga nyumba yayikulu yopemphereramo m'dayosizi ya Karonga yayamba ndipo ikuyembekezeka kudzatha mu Julaye chaka cha mawa, pakutha pa miyezi isanu ndi yitatu, Mkwaso wapeza.

Malingana ndi momwe Mkwaso wauziridwa, nyumbayi izidzatchedwa St. Joseph the Worker Cathedral.

Dayosiyi ya Karonga yomwe idakhazikitsidwa pa 20 Novembala chaka cha 2010 ndi mtumiki woyera Benedict XVI, ndipo yili pansi pa utsogoleri wa ambuye Martin Mtumbuka, ikugwiritsa tchalichi cha pa parishi ya St. Annes m'boma la Karonga ngati Cathedral yongogwirizira.

"Tikukhulupirira kuti pakutha kwa miyezi yitatu ndi yisanu ntchito yomanga tchalitchichi yidzakhala itatha. Tili n'chikhulupiriro kuti anthu akufuna kwabwino apitiriza kutithandiza mpakana pamene ntchitoyi idzathere makamaka mwezi wa Julaye chaka cha mawa," adatero Bambo Charles Chinula omwe ndi woyang'anira momwe chuma chikuyendera m'dayosiziyi.

 



@2010 The Maravi Post an Eltas EnterPrises INC Publishing Company
Site Developed By JRC

Top Desktop version