The Maravi Post

Switch to desktop Register LoginChipani chosutsa cha DPP chilandidwa ofesi ku Balaka

MZUZU--Chipani cholamula cha People's Party (PP) chalanda ofesi chipani chosutsa cha Democratic Progressive Party (DPP) m'boma la Balaka mosatsatira malamulo, MaraPost yadziwa.

Bwanamkumbwa wa m'boma la Balaka a Rodrick Mateauma avomereza kuti sakudziwa momwe chipani cha PP chidalowera mu maofesiwo omwe bomali limafuna kuti akatswiri osunga chuma a Malawi Savings Bank adzigwiritsa ntchito.

A Mateauma adati padakali pano ayisiya nkhaniyi m'manja mwa unduna woyang'anira za m'maboma ndi chitukuko cha kumidzi.

Malingana ndi mkuluyu, chipani cha DPP sichimapereka lendi koma chitachoka m'boma kutsatira imfa ya pulezidenti Bingu wa Mutharika ofesi yake idalembera chipanichi kuti chilipire ndipo chidatero.

Wapampando wa chipani cha PP ku Balaka a Mussa Jangali adauza wayilesi ya ZBS kuti adalowadi m'maofesiwo koma sanathe kulongosola ngati chipani chawo chidatsata ndondomeko zoyenera.Tags: DPP  

@2010 The Maravi Post an Eltas EnterPrises INC Publishing Company
Site Developed By JRC

Top Desktop version