The Maravi Post

Switch to desktop Register Login



Kuthawa msonkho kukulepheretsa MRA kutolela mokwanira

MZUZU--Bungwe lotolela msonkho la Malawi Revenue Authority (MRA) lati khalidwe lothawa kulipira msonkho likupangitsa kuti asamatolele ndalama zokwanira.

Malingana ndi malipoti, MRA idalephera kukwanitsa kutolela ndalama zokwanira m'mwezi wa Disembala chaka chatha. Bungweli lidatolela ndalama zokwana K7.86 biliyoni zokha m'mweziwu m'malo mwa K8.1 biliyoni yomwe lidayenera kutolela.

Mneneri wa bungwe la MRA a Steve Kapoloma adakana kuyankhulapo pa katoleledwe ka msonkho chaka chatha koma adati limodzi mwa gwero la vutoli ndi kuthawa msonkho.

"Ambiri akumathawa kulipira msonkho zomwe zikupangitsa kuti tisamatolele mokwanira," a Kapoloma adauza nyuzipepala ya The Nation.

Koma katswiri wina wa zachuma a James Nyirenda adati bungwe la MRA likulephera kutolela mokwanira chifukwa choti makampani ambiri m'dziko muno sakupindula m'malonda awo.

"Makampani akuvutika chifukwa cha zinthu zambiri zomwe zikukwera m'dziko muno. M'chitidwewu ukupangitsa kuti makampaniwa asamapange phindu m'malonda awo," adatero a Nyirenda.



Tags: MRA  

@2010 The Maravi Post an Eltas EnterPrises INC Publishing Company
Site Developed By JRC

Top Desktop version