The Maravi Post

Switch to desktop Register LoginMoyo pa Malawi kuwawa: Thumba la chimanga lafika pa K7 500

Moyo kuwawa ku MalawiMZUZU--Thumba la makilogilamu makumi asanu lafika pa mtengo wa K7 500 m'madera ambiri a m'dziko muno kuchokera pa mtengo wakale wa K5 000, kafukufuku wa Marapost wasonyeza.

 Izi akuti zadza kamba ka kugwetsedwa mphamvu kwa ndalama ya kwacha mwezi wa Meyi chaka chatha komanso chifukwa choti chimanga chomwe chimagulidwa pa mtengo wa K3 000 mulingo omwewu ku Agricultural Development for Marketing and Corporation (ADMARC) chikusowa.

Malingana ndi kafukufuku wa Marapost, mtengowu ndi womwe anthu akugulira m'madera ambiri ku Mzuzu, Nkhotakota, Blantyre ndi ku likulu kwa dziko lino ku Lilongwe.

Chaka chatha bungwe loonera momwe anthu akukhalira m'dziko lino la Centre for Social Concern (CfSC) lidaonetsa kuti banja la anthu asanu limayenera kukhala ndi ndalama zoposera K88 000 kupatula ndalama za mayendedwe, zovala ndi zolipira ana sukulu kuti likhale mopanda mavuto m'mzinda wa Lilongwe.

Tags: Malawi  Chimanga  

@2010 The Maravi Post an Eltas EnterPrises INC Publishing Company
Site Developed By JRC

Top Desktop version