Written by YAMIKANI SIMUTOWE
BLANTYRE (BLANTYRE) -- Bungwe la Public Affairs Committee, lomwe limalimbikitsa ulamuliro wabwino komaso ufulu wachibadidwe mdziko la Malawi, lati liwunguza ndi kufufuza anthu onse amene akufuna kuzapikisanawo pa chisankho cha mtsogoleri wa dziko ngati m’modzi wa iwo adzatumikiredi aMalawi atapambana pa chisankho chomwe chichitike chaka cha mawa.
Written by YAMIKANI SIMUTOWE
BLANTYRE (MaraPost) -- Chipani cholamula mdziko la Malawi cha People’s Party (PP) chathira mphepo a John Kapito yemwe ndi mkulu wa bungwe la Consumers Association of Malawi (Cama) kamba kokhala chete osaumiliza anthu amalonda kuti atsitse mitengo yogulitsira katundu wawo kutsatira kutsika kwa mtengo wa mafuta mdzikomo.
Written by PIUS NYONDO
MZUZU (MaraPost) -- Dzina lake ndi Kondwani Hara. Ali ndi zaka 13. Alemba mayeso ake a Sitandade 8 pasukulu ya pulayimale ya Lulindo ndipo ali ndi chikhulupiliro kuti asankhidwa kuti apite ku sekondale yogonera komweko zotsatira za mayeso zikatuluka.
Written by PIUS NYONDO
MZUZU (MaraPost) -- Mayiko ndi mabungwe othandiza dziko lino pa zachuma ati ali ndi nkhawa pa zomwe mtsogoleri wa dziko lino a Joyce Banda adanena kuti atengera ndondomeko yoyendetsera za malo ya ku Zimbabwe kuti aMalawi apindule.
Written by PIUS NYONDO
MZUZU (MaraPost) --Kusowa kwa malo okwanira bwino mu muzinda wa Lilongwe kwapangitsa kuti chipani chakale cholamula cha Malawi Congress Party (MCP) chisunthe tsiku la msonkhano wake waukulu omwe umayenera kuchitika sabata yino kuyambira pa 27 mpakana pa 29 Epulo.
Hits: 1514