Site icon The Maravi Post

Banja la Mia, MCP igawa ma Masiki kwa ochita malonda ku Blantyre

MCP official donating facemask to Blantyre traders

BLANTYRE-(MaraviPost)-Chipani cha Kongeresi kudzera mu nthambi yake yowona zotsamalira anthu, masana wa Lachiwiri chapereka tinsalu totchingira pakamwa ndi mphuno totchedwa ‘fesi masiki’ kwa mavenda omwe amachita malonda mu msika wa mu mzinda wa Blantyre.

M’malo mwa chipani cha Kongeresi, Wachiwiri kwa mkulu woona zotsamalira anthu m’chipanichi, a Lawrence Malemia ndi omwe anapereka ma masikiwo kwa akuluakulu a mu msikawo.

Izi zatheka kamba ka banja la a Mia motsogozedwa ndi olemekezeka Mayi Abida Mia omwe ndi wachiwiri kwa nduna yowona za malo komanso phungu wa dela la Chikwawa Nkombedzi.

Banja la a Mia lapereka zipangizozi ku chipani cha Kongeresi kuti chifikire magulu osiyanasiyana ndi cholinga choteteza anthu ku mliri wa matenda a Covid 19 omwe ukupitilirabe kuchotsa miyoyo ya anthu ochuruka.

Masiku apitawa, banja la a Mia ladapereka ma masiki a nkhaninkhani ku chipani cha Kongeresi ndipo ndi thandidzoli, chipanichi chafikila kale akaidi ndi ogwira ntchito ku ndende mu ndende zosiyanasiyana m’chigawo cha kum’mwera kwa dziko lino la Malawi.

Banja la a Mia lidaperekanso makina osokera oposa 50 ndi ma litaka a nsalu kwa atsogoleri a ndale kuti akagwiritse ntchito yosoka ma masiki ku madera awo osiyanasiyana.

Mu mwezi wa Januwale chaka chino, banja la a Mia komanso boma la Malawi pamodzi ndi anthu a m’dziko muno adali pa chisoni chachikulu chifukwa cha imfa ya malemu Muhammed Sidik Mia yemwe adali wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Kongeresi, nduna ya boma, wandale wotchuka komanso katakwe pa nkhani za bizinesi.

Malemu Mia adamwalira atadwala matenda a Covid 19.

The Maravi Post has over one billion views since its inception in December of 2009. Viewed in over 100 countries Follow US: Twitter @maravipost Facebook Page : maravipost Instagram: maravipost    
FacebookTwitterEmailWhatsAppShare
Exit mobile version