
Minister of information, Civic Education and Communications Technology, Mark Botomani, MP, Wednesday, 27th November 2019, said government is working tirelessly together with other institutions in improving postal services.
He said this during the commemoration of World Post Day in Nkhotakota
FULL SPEECH IN CHICHEWA BELOW
Moni nonse, Muli bwanji
Choyambirira ndithokoze mafumu ndi anthu anu potilandira m’mudzi muno.
Tasonkhana pano lero kuti tikumbukire ntchito zama Post Office ndi mabungwe ena omwe amatumiza lamya, mauthenga komanso kalata.
Ndikhulupilira tonse tikudziwa ntchito zomwe ma post office amagwira.
Mafoniwa asanabwere, ambirife timadalira ma post office kuti titumize uthenga kwa achibale kapena amzathu. Timakaposita kalata ija ndiye imatenga masiku ndithu kuti ikafike. Ikafika, amatiyankhanso.
Ena mmalo motumiza kalata, amakaimba foni ku post office. Lero mafoni ali paliponse ndipo zopita kukaimba foni ku post office zachepa. Chitukuko chapita patsogolo.
Palinso makampani ambiri omwe akugwira ntchito zotumiza mauthenga, katundu ndi kalata. Onsewa cholinga chawo ndi chimodzi —kupititsa patsogolo chitukuko cha dziko lathu lino.
Ntchito za lamya zinayamba kalekale tonse pano tisanabadwe. Tsikuli timalikumbukira pa 9 Okotobala chaka chilichonse koma chaka chino kuno kwathu tikulikumbukira lero pa 27 November.
Amayi ndi Abambo, ntchito za lamya zathandiza kutukula maiko ambiri. Inu mukudziwa bwino kuti mauthenga ndi ofunikira kwambiri pamoyo wa munthu. Mauthenga amatithandiza kutiongolera mmene tiyenera kuchitira zinthu. Mauthenga amatithandiza kuti titenge nawo gawo pachitukuko cha dziko.
Maiko amakondwelera tsikuli munjira zosiyanasiyana. Mmaiko ena, mabungwe omwe amagwira ntchito za lamya amakonza mipikisano ya zolembalemba; ena amathandiza pachitukuko cha dziko monga kumanga sukulu.
Kwathu kuno, bungwe la MACRA lamanga zipinda zophunziriramo ndipo lero kuno ku Malawi tikukondwelera tsikuli podzapereka zipinda zimenezi ku sukulu ya Maungu.
Ine monga ngati nduna yoyanganira zintchito za Lamya ndi ma positi, ndikufuna ndithokoze bungwe la MACRA ndi ma bungwe onse amene agwira ntchito yotamandika pa school pano.
Pamalo pano panalibe school yolodzeka. Ana amaphunzira muzisakasa. Koma lero taonani pabwera ma block okongola ngakhale mvula itagwa motani, ana sangavutike kukhalamo, apitiliza maphunziro awo bwinobwino.
Ma block amenewa akhala ndi ma desk mbambande! Komanso, aphunzitsi kuti ntchito yawo iyende bwino amayenela akhale ndi office.
Komanso zimbuzi ndi zofunika kwambiri pa moyo wa ana pamene ali pa school. Ndiye anzathuwa atimangilanso zimbuzi zinayi.
M’manjamo!!!!!
School ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo wa munthu ndipo zomwe zachitika pamalo pano, ndi chiyembekezo chachikulu kwa makolo ndi ana am’mudzi muno pankhani ya tsogolo lawo.
Bwana DC, tikupempheni kuti mukhale maso athu pa school imeneyi. Ife timakhala kutali. Tikufuna m’mudzi muno mudzatuluke DC kutsogoloku ngati inuyo.
M’manjamo!!!
Ndiye chonde athandizeni msanga pa zomwe zisowe upangiri wanu kuti chilichonse chiziyenda bwino. Ndipemphenso ana asukulu, makolo ndi anthu onse ozungulila sukuluyi kuti chonde isamaleni.
Mwapadela ndithokoze anthu a m’mudzi muno chifukwa chakudzipereka kwanu. Ntchito imeneyi siikanayenda kopanda inu.
Munathandiza kwambiri poumba njerwa, kututa mchenga ndi kutungira madzi.
Izi zikutsonyeza chidwi chomwe muli nacho pa maphunziro a ana anu. Tikuti zikomo.
Choncho ndikulimbikiseni kuti musabwerere mbuyo, koma pitilizani kutumiza ana anu ku school popeza kuti maphunziro ndi chiyambi chothetsa umphawi pa moyo wamunthu.
Ana mukuwaona apawa kuti azakhale Minister kapena nduna kutsogoloku afunika school. Choncho school ndi chida chachikulu pa chitukuko cha dziko lathu la Malawi.
Ndi mau amenewa, zipinda zatsopano zomwe bungwe la MACRA lamanga tsopano dzaperekedwa ku sukulu ino ya Maungu lero pa 27 November 2019.
Ambuye akudalitseni.
Zikomo