LILONGWE-(MaraviPost)-Bwalo lalikulu la mfumu Masula ku Lilongwe lapeza wolakwa a Divason Vaison ndi MacCloud Duwe pochita zaukambelembele pa malo amalemu Lingson Belekanyama.
Kotelero kuti bwaloli lalamula kuti 7 acres yomwe a Davison ndi a Duweh adagulitsa kwa a Chadza libwelele kwa ana amalemu Belelanyama.
Malinga ndichigamulo chomwe chaperekedwa lachiwiri pa January 9, 2024 mfumu Masula lidapeza olakwa a Davison omwe adatenga ndalama kwa malemu malo a Belekanyama omweso adakatenga ndalama zina kwa Chadza pamalo amodzi.
Malinga ndi kafukufuku pankhaniyi pakuoneka kuti a Duwe ndi womwe adapeza ogula malowa ndipo adapanga upandu ogulitsa malowa.
Kotero kuti bwalo la mfumu Masula ladzuzula mchitidwe waupandu ndi wakuba omwe a Duwe ndi a Davison adachita.
Malemu Belelekanyama anali phungu wakunyumba ya malamulo ya Lilongwe Nsinja.
Malemu Belelekanyama natisiya mchaka cha 2020.