Site icon The Maravi Post

Mlandu wokhuza chisankho ku Mangochi Monkeybay upitirira  pa 5 August

Mlandu wokhuza chisankho ku Mangochi Monkeybay upitirira  pa 5 August

 

Wolemba; Leo MKHUWALA

Bwalo la milandu la High Court mu mzinda wa Blantyre Lachinayi layimitsa mlandu wokhuza kusavomereza zotsatira za chisankho womwe adakamang’ala ku bwaloli ndi m’modzi wa anthu omwe  adapikitsana nawo pa mpando wa phungu m’dera la Mangochi Monkeybay poimila chipani cha Malawi Congress Party (MCP), a Gerald Kazembe.

Poimitsa, mwa zina, Jaji yemwe akumva mlanduwo, Maclean Kamwambe anati waimitsa mlanduwo pofuna kupereka mpata kwa maloya omwe akuimila bungwe lowona za chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) kuti akhale ndi nthawi yokwanila yobweretsa kubwaloli ma umboni a zikalata zomwe padalembedwa zotsatira za chisankho.

Jaji Kamwambe anapanga ganizo loyimitsa mlandu potsatira pempho la maloya a MEC omwe anapempha nthawi yokwanira.

Angakhale anamitsa mlanduyo mpaka pa 5 August, Jaji Kamwambe anapereka chenjezo kuti salola kuti papitilire kukhala kuchedwa kulikonse pa mlanduwu.

Malinga ndi ndondomeko ya bwalo, Lachinayi pa 18 July limayenela kukhala tsiku lomwe ena mwa akulu akulu omwe amayendetsa chisankho monga ma Presiding Officers amayenela kufunsidwa mafunso ndi loya yemwe akuimila odandaula, a Patience Maliwa omwe amagwira ntchito ku kampani ya maloya yotchedwa Icon and Company.

Motsutsana ndi ndondomeko ya bwalo, zinadziwika kuti ma Presiding Officer omwe amayenera kufika kubwalo lamilandu sanafike.

Wodandaula, a Gerald Kazembe omwenso ndi wotsatira kwa mkulu woona zotsamalira anthu m’chipani cha MCP, adakagwada ku bwalo lamilandu pofuna kuti bwalo liunikire momwe chisankho m’dera la Mangochi Monkeybay chidayendera.

Kudzera mwa owaimilira pa mlandu, a Kazembe adavomera kuti maloya awo apemphe bwalo kuti linene kuti zotsatila za chisankho cha phungu chomwe chidachitika m’dera lawo pa 21 Meyi nzopanda ntchito.

Mwa zifukwa za kholophethe, a Kazembe adapeza kuti kuchuruka kwa anthu m’malo ena momwe adaponyeramo voti kunkapyola chiwerengo cha anthu omwe adali mu kaundula woti angathe kuponya voti. Iwo adapezanso kuti ena mwa akulu akulu oyendetsa chisankho ankatengera kunyumba kwawo zipepala za zotsatira za chisankho ndipo pobwelera nazo zimakhala zitafutidwa ndi utoto wofutila manambala ndi zilembo wotchedwa kuti tipp-ex.

Potengera zotsatira za chisankho chomwe chidali ndi madando ochuruka, bungwe la MEC lidalengeza kuti yemwe ankapikitsana nawo pa mpando wa phungu poimila chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) a Ralph Jooma omwenso pakadali pano ndi nduna yowona za Mtengamtenga ndi omwe adapambana.

The Maravi Post has over one billion views since its inception in December of 2009. Viewed in over 100 countries Follow US: Twitter @maravipost Facebook Page : maravipost Instagram: maravipost    
Exit mobile version