LILONGWE (MaraPost)—Prophet Austin Liabunya wauza dziko la Malawi pa yemwe adzapambane Chisankho chimene chili nkudza miyezi ikubwelayi pa 20 May 2014. Mtumiki wa Mulunguyu wanena izi pa wayilesi ya Galaxy FM dzulo pamene amafotokoza za Mapemphero amene anakoza olowera Mchakacha chtsopanochi amene anachitikira ku Area 23, mu Mzinda wa Lilongwe. Prophet Liabunya anacheza ndi Mtolankhani wa Galaxy radio bambo Gerald Viola motere.
GVIOLA: Kodi inu ndamva mumalosera, chiyambireni Ulosiwanu zoonadi zidachitika ndiziti?
PROPHET: Zonse zomwe ndimalosera zimachitika chifukwa samakhala ine onenayo koma Mulungu. Ndinali woyamba kulosera za Imfa ya Mtsogoleri wadzikolino pa 12 November 2011 koma anthu anati ndinali wamisala.Ndinafotokozanso za mmene Ulamuliro umayenera kuyendera kuti anthu ena adzafuna kuti woyenera kulowa pa Udindo wa President asalowe komabe sizidzatheka malinga ndi malamulo, izi zinachitika ndithu.
GVIOLA: Anthu ena akuti inuyo posachedwapa mwatulusa Ulosi wanu, kodi ukuti bwanji Ulosi umenewu:
PROPHET: Ulosiwu ndinaunena mu October wa 2013 mpaka 2016. Ulosiwu ukunena za mavuto omwe aMalawi akhale akukumana nao oposa nthawi ya Mmbuyomu pamene tiri ndi Utsogoleri ulipowu ndipo anthu adzauchotsa Utsogoleri ulipowu okha kudzera pa voti. Komanso ndikufotokoza zambiri mpaka 2016 za momwe zinthu zikhalire nchaka cha 2014 chifukwa Chipani china pomafika nthawi ya Chisankha chidzakhala ndi Nkhope zanyowani zokhazokha onse alipo odziwikawa atachoka.
GVIOLA: Tinamva kuti inu munalosera zakuchoka kwa Vice President wina wa Chipani ndikuti Vice Presidentyo akakalowa Chipani, Chipanicho chikawina Chisankho, kodi izi ndizoona?
Yes, ndinaloseradi zimenezo ndipo aMalawi ndi Mboni. Palibe Vice President wacHipani yemwe wachoka panopa?
GVIOLA: Mukunena Wolemekezeka a Cassim Chilumpha kapena?
PROPHET: Mulungu amandiuza zomwe anthu angakumanenazo munyengo inayake ndiye za Chilumpha sindidatchule dzina, Anthuo ndimaaonatu mmaso mwangamu koma sindingaatchule maina koma zonse ndimalosera zikutsatizidwa.
GVIOLA: Inutu mwina mukuphatikiza ndi Using’anga inu? Mumadziwa bwanji zakutsogolo?
PROPHET: KKKKKK Nanga Uzimu tingauphatikize bwanji ndi Using’anga? Nzosatheka zimenezo.
Mulungu amandiunikira ndiye ndimalankhula pofuna kuchenjeza anthu kuti akonze zomwe akulakwitsa zija ndiye ngati anthu sasintha amakumanadi ndi zokhoma zija koma Mulungu amafuna kuti munthu uja asinthe moyo wake, safuna kuti munthu apeze mavuto ayi ndithu ,mwachitsanzo: Ngati ulosi ungati udzagundidwa ndi galimoto, ukuyenera kupewa ngoziyo pokonza mtimawako. Mulungu samgafune kuti ugundidwe ndi galimoto, koma ngoziyo imachitikabe pamene iwe wapulumuka ngati unasintha kayendetsedwe ka moyo wako.
GVIOLA: Ngatidi inuyo mukutumidwa ndi Mulungu kuti muzilosera, yemwe apambane Upresident mChisankho cha chaka cha Mawa ndani?
PROPHET: Yemwe apambane ndi amene mbalewake anakhalapo kale President mMalawimuno.
GVIOLA: Mwati yemwe bamboake anakhalapo kale pa Mpando wa Upresident?
PROPHET: A Viola, ndati yemwe mbalewake anakhalapo kale President ndiyemwe awine chaka cha mawa, zambiri ndikanena ku Area 23 ku Cross Over Service, anthu abwere mwaunyinjiwao adzamve zomwe Mulungu akawayankhule zokhudza moyowao ndizokhuza Dzikolao.
Discover more from
Subscribe to get the latest posts sent to your email.