BLANTYRE-(MaraviPost)-First Vice President wadziko lino Jane Ansah walimbikitsa azimayi onse m’dziko muno kuti azidalira komanso kumuuza Mulungu akakumana ndi zovuta kapena zopinga zina zilizonse m’moyo wawo osati kufalitsa ma unthenga kuzela mumatsamba anchezo kapena kuuza anthu zamavuto awo ponena kuti zimenezi sizimapindula kanthu kena kalikonse.
Pogwirizana ndi mutu wa msonkhano wa amayi a mpingo wa Zambezi omwe unachitikira kwa Manjawira m’boma la Ntcheu wonena kuti ”Muchipululu simofwera”, Dr Ansah anati azimayi akuyenera kumadalira Mulungu wakumwamba. Iye ananenanso kuti mavuto angachuluke bwanji, limafika tsiku limene amatha.
Dr Ansah anauza azimayiwa kuti azilimbikira kugwira ntchito zachifundo komanso kutumikira moyenera m’mabanja awo.
Mu uthenga wake womaliza, Dr Ansah anauza azimayiwo kuti azilola chipembedzo kukhala chida chowayanjanitsa komanso kukhala ogwirizana, monga momwe mtsogoleri wadziko lino, Professor Arthur Peter Mutharika, amalimbikitsira za umodzi m’dziko muno.