Site icon The Maravi Post

Vera Chilewani Adzaimila MCP Kumpoto Cha Kum’mawa Kwa Blantyre

Vera Chilewani Adzaimila

Chipani cha Kongeresi chasankha Mayi Vera Chilewani kuti adzaimire chipanichi ngati phungu wake m’dela la kumpoto cha kum’mawa kwa boma la Blantyre pa chisankho chomwe chichitike chaka chamawa.
Chikhwimbi cha anthu otsatira chipanichi chawasankha a Chilewani popanda wopikisana naye.
Malinga ndi zomwe wolemba nkhani wathu wapeza, anthu a m’derali ndi wokondwa kuvomereza Mayi Chilewani kuti adzawaimire pa chisankho cha patatu ataona zipatso za utsogoleri zomwe mayiyu ali nazo.
“Ndi Mayi wachikondi komanso wochangalama pogwira ntchito za chitukuko ndipo sitikukaika kuti dela lino lidzatukuka akakhala phungu m’mwezi wathu miyezi ikudzayi,” anafotokoza motero  bambo wina chimwemwe chiri tsaya kusimba za a Chilewani.
“Ifetu tikuchiona chamwayi kukhala ndi munthu wamayi kuti atitsogolere ngati phungu  chifukwa mayi akakhala mtsogoleri makamaka phungu amakhala mlera khungwa,” anatero powonjezera.
M’mawu awo, a Chilewani anati ndi wokondwa kuti anthu m’chipanichi awapatsa mwayi kuti awatsogolere pambuyo powona mwa iwo zipatso zabwino maka pa nkhani za chitukuko.
Mayi Chilewani omwe m’mbuyomu adakhalapo phungu wa m’boma la Nsanje ndi mayi wachiwiri kupambana pa chisankho cha chipulula m’chipani cha Kongeresi m’chigawo cha kum’mwera.
Masiku apitawa, chikhwimbi cha anthu otsatira chipani cha Kongeresi anasankha mkadzi wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipanichi, Mayi Abida Mia kuti adzaimire chipanichi m’dera la Chikwawa Mkombedzi.
Chimodzimodzi ngati Mayi Chilewani, Mayi Mia adalibe wopikisana nawo.
The Maravi Post has over one billion views since its inception in December of 2009. Viewed in over 100 countries Follow US: Twitter @maravipost Facebook Page : maravipost Instagram: maravipost    
FacebookTwitterEmailWhatsAppShare
Exit mobile version