Chakwera wati utsogoleri wake ukuyesetsa kuthana ndi mavuto mdziko muno

By Kondanani Chilimunthaka

Mtsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera, yemwenso ndi mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress wati akuzindikira kuti aMalawi ambiri akupysinjika ndi mavuto ochuluka kamba ka kukwera mtengo kwa katundu, komanso kusakhala ndi mwayi opeza ngongole mthumba la NEEF, koma iye wati boma lake likuchita chotheka kuti zonse zikhale mmalo mwake ndipo kuti aMalawi ayambe kuona kusintha.

Chakwera amalankhula izi lachiwiri pa 2 Sepitembala, 2025 pomwe anayima pa sitolo za Mpingu mdera la Likuni m’boma la Lilongwe pa ulendo wake ochititsa misonkhano yoyimayima pokopa anthu kuti adzavotere chipani cha Malawi Congress pachisankho cha pa Sepitembala 16.

Mtsogoleri wa dziko linoyu wati katundu wina wayamba kale kutsika mtengo kamba koti boma layamba kukonza zomwe zimapangitsa kukwera mtengo kwa zinthu mdziko muno.

Mmau ake amene akuyimira dera la Likuni pa mpando wa phungu mchipani cha Malawi Congress, Jean Muonaowawuza Sendeza, anati mafumu ndi othokoza kuti Pulezidenti Chakwera m’mbuyomu adapitanso kukalimbikitsa anthu kulembetsa mkuwundula wa chisankho, ndipo anati anthu omwe ndi pafupifupi 44,000 akonzeka kukavotera chipani cha Malawi Congress tsiku la chisankhochi.

Sendeza wathokozanso utsogoleri wa Pulezidenti Chakwera kamba ka zitukuko monga madzi a mmipope, nyumba zamakono za apolisi, komanso zitukuko zina zomwe boma lachita mdera la Likuni.

Nayo mfumu yayikulu Bwatalika ya mderali inathokoza Chakwera kamba kolimbikitsa umodzi mdziko muno, ndipo yati ichi ndi chimodzi mwa zifukwa zimene aMalawi ambiri adzavoterenso mtsogoleriyu pa Sepitembala 16.

Pulezidenti Chakwera lero akuchititsa misonkhano yoyimayima m’maboma a Lilongwe ndi Mchinji.