Malawi Politics

“Kuthandiza azibusa ndi ngongole ya NEEF ndizabwino koma achinyamatawa zikuvuta pati apeze nawo mwayi?”-Dr Kabambe

2 Min Read

LILONGWE-(MaraviPost)-Mtsogoleri wachipani cha UTM wadzudzula boma posawapatsa achinyamata mwayi wangongole kudzera ku bungwe la NEEF pamene boma lomweli lapatsa azibusa ngongole yokwana MK8.4 billion.

Dr Kabambe akuti kupereka ngongole kwa azibusa sikolakwika koma kusalidwa kwa achinyamata pofuna kupeza thandizo ngati lomweli.

Mtsogoleri walemba izi pa tsamba lake la mchezo motere…..

Ndaona achinyamata angapo akulemba zodandaula ndalama zomwe a NEEF apereka kwa azibusa zokwana K8.4 billion, sizolakwika koma dandaulo lawo likudza poti NEEF yomweyo iwowo akapita kuti abwereke ndalama apangire business akumawakana. Chinanso chodandaulitsa ndi default rate ya azibusa analandira ndalamazo pomwe zadziwika kuti over 80% ya azibusawo anangolandira ndalamazo nkudya sanabwenze. K8.4 billion yangolowa mmadzi.

Ena angapo ndaona anafika pogawa ntchito zomwe K8.4 billion ikanagwira, ena akamba za ma fakitale, akuti mukanawapatsa achinyamata akanatha kutsegula ma fakitale 10, ya K840 million each mma dera awo opanga zosiyanasiyana monga furniture, za technology, mafuta ophikira, soap, zakumwa, ndi zina zambiri. Ndipo amaunikira kuti akanatha kulemba ntchito achinyamata amzawo oposa 1000, kubweretsa revenue kuboma, kupanga create ma business kwa achinyamata ena. Mfundo zomveka, zakuya.

Ndimati ndinene ichi mogwirizana nanu. Pomwe talephera amalawi ndipomatenga ndalama zathu nkumayika mmanja moti sizipindula kanthu, angothera kudyera, kuyendera. Manja ambiri aluso sitiwapanga support, mpaka mayiko ena amabwera nkuwatenga nkumakapindula nawo. Lero tikuvutika ndi magetsi yet dziko lino linali ndi William Kamkwamba, mnyamata yemwe anatha kupanga magetsi kuchokera kumphepo, ngati dziko we failed to finance the project, tikanapanga finance the idea sitikanangopeza magetsi okha, tikanapedzanso ntchito, ma business, komanso revenue kudzera mmisonkho, zitsanzo nzambiri inunso muli nazo

Koma vuto ili latha. Simudzadandaulanso za K8.4 billion, ife chaka ndi chaka tidzipereka K500 billion ku ntchito za mafakitale, kutsegula mafakitale atsopano komanso kukhazikitsa ndondomeko zogwiritsa ntchito njira zamakono kuti mafakitale amenewa azipanga katundu wabwino ndiponso wamakono. Izi ndi zomwe tidzakhale tikupanga chaka chili chonse kwa zaka zisanu. We will finance ma ideas ngati amenewa. Mmaboma onse kuchokera ku Nsanje mpaka ku Chitipa mudzakhala ma fakitale opanga zosiyanasiyana amene adzapange bridge gap ya production, nkutichepetsera importation, napanga create millions of job and business opportunities, oyendetsedwa ndi amalawi, owned by Malawians, ndalama zidzakhala ndi amalawi ndipo zomathawa mma district kumapita mma city zidzatha. Ma district adzakhala ndi plenty of opportunities enanso tidzachoka mmatauni kumabwelera mmakwathu kukatukula kwathu.

Iyiyi si nthano, izizi zichitika in real time mukativotera. Amalawi kusintha Boma sikanthu, koma kuvotera munthu wamzeru, waluntha, wachidwi ndi mavuto athu. Yehova anatikonda 2019 potipatsa Biyeni, koma sitinampatse mpata owina zisankho, watikondanso ulendo uno, don’t repeat the mistake we made in 2019. Vote yanu perekani kwa Dr. Kabambe ngati mukufuna Malawi otukuka, otsogola

TsogoloLowalaWithDrDalitsoKabambe

MalawiWatsopanoNdiwotheka