MZUZU (MaraviPost) — Nduna ya za Umoyo a Jean Kalirani ati m’pofunika kuti anamwino ndi azamba ophunzira kwambiri azipezekanso m’zipatala za m’madera osiyanasiyana m’dziko lino.
A Kalirani adanena izi ku Lilongwe malingana ndi mchitidwe womwe akadaulo a za umoyo amakhala nawo womakagwira ntchito m’mayiko ena makamaka ku Mangalande ndi ku Jobeki.
“Tikufuna kuti anamwino ndi azamba omwe ali ndi maphunziro opitirira Masitazi azikhala akugwira ntchito yowonetsetsa kuti odwala akuyang’aniridwa mwaluntha,” adatero a Kalirani.
Iwo adati zoterezi zizapangitsa kuti ena amaphunziro ocheperapo azikhala ndi utsogoleri wabwino akamagwira ntchito.