Wolemba: Robert Linje
LILONGWE-(MaraviPost)-Mmodzi mwa a katswiri pankhani zamalamulo mdziko muno a George Jivason Kadzipatike, alengeza kuti akapikisana nawo paudindo wa mlangizi wamkulu pankhani za malamulo ku chipani cha Malawi Congress (MCP).
A Kadzipatike omwe amadziwika kwambiri kuti ‘Jivason’ ati ganizoli ladza pofuna kulimbikitsa nthambi yazamalamulo muchipanichi ndipo amema nthumwi kuti zikaavotere ku msonkhano waukulu omwe chipanichi chichititse pa 8 August, 2024 ku BICC mu mzinda wa Lilongwe.
A Kadzipatike ndi katswiri pankhani yamalamulo, kuyimila anthu, mabungwe komanso nthambi zaboma pamilandu, pomweso akhala akudzipereka pothandiza ntchito zachipani cha wanthu, chipani cha MCP mwaulere.
Iwo adachita maphunziro a ukachenjede pankhani zamalamulo a Masters komanso Degree yoyamba pankhani zamalamulo ku sukulu ya ukachenjede ya Unima.
Ndi katswiri ovemerezeka ndi boma pokhalira mboni, yoonetesetsa kuti anthu sakuchita chinyengo. Alinso ndi chiphaso chogwilira ntchito zamalamulo m’mabwalo onse amilandu mdziko muno komanso akunja.
A Kadzipatike akhala akuyimila anthu pa milandu kwa zaka zoposera 15, kamba ka ichi iwo akubweretsa ukadaulo wapaderadera pankhani zamalamulo ku chipani chokondeka cha MCP.
M’mbuyomu akhala akuthandiza chipani popereka mphatso zosiyanasiyana monga galimoto, zomwe zakhala zikuthandizira ntchito zachipani.
Iwo akulonjeza kuti azakhala patsogolo kulimbikitsa mamembala a chipani kutsatira komanso kusunga ngodya zinayi zachipanichi za Umodzi, Kukhulupirika, Kumvera ndi Kusunga Mwambo.
“Pamene ndikupitiliza ntchito yanga yoyimila anthu, mabungwe ndi makampani pamilandu kumabwalo kudzera mukampani ya Jivason and Company, ndaganiza zopikisana nawo paudindo wa mlangizi wamkulu pankhani za malamulo muchipani cha MCP ngati njira imodzi yotumikira chipani ndi mamembala ake. Ndizachita izi modzipereka,” atero aka Kadzipatike.
Kuonjezera paukatswiri wake pankhani za malamulo, Kadzipatike ndi munthu odalilika, odzipereka, okhulupirika komanso odzichepetsa yemwe wakhala akupereka mathandizo osiyanasiyana kuchipani kuphatikizapo galimoto zomwe zakhala zikuthandiza pantchito zachipani.
Kwa zaka zambiri akhala akuimira chipani cha MCP komanso boma pamilandu yosiyanasiyana kumabwalo a milandu poonetsa chikondi komanso kudzipereka komwe alinako kuchipani
Zina mwa mfundo zomwe katswiriyu akulonjeza ngati nthumwi zachipani zingaasankhe paudindowu ndiogwiritsa ntchito zipangizo zake, chuma chake, magalimoto komanso ogwira ntchito a kampani yake mwaulere kugwira ntchito zachipani.
A Kadzipatike ati iwo pokhala paudindo wa mlangizi wamkulu pankhani za malamulo ku chipani cha MCP, chipanichi chikhale chotsimikizika kukhala mmodzi wamakasitomala ofunika kwambiri a kampani yawo ya Jivason and Company.
Kotero iwo ati mogwirizana ndi akatswiri ena pankhani zamalamulo komanso akuluakulu a chipani, azachilimika komanso kukangalika pokhazikitsa nthambi yamphamvu pankhani zamalamulo mu chipani cha wanthu cha MCP.
“Ife ngati a Malawi, tidabadwa a Kongeresi, nkona nthawi yakwana tsopano kuti ndithandize chipani chathuchi munjira ina Pokhala mmodzi mwaakuluakulu muchipanichi,” iwo anaonjezera motero.
Akasankhidwa paudindo wamlangizi wamkulu pankhani za malamulo muchipani cha MCP, a Kadzipatike alonjeza kupititsa patsogolo zofuna zachipanichi komanso kutsogolera kukhazikitsa ndondomeko zapamwamba pankhani zamalamulo zokomera chipani.
Iwo atsimikizanso kuti chipani cha MCP chidzakhala chimodzi mwamabungwe ndi ma kampani omwe iwo amawayimila pamilandu.
Ganizo la a Kadzipatike lofuna kupikisana nawo paudindowu , likuonetseratu poyera kudzipereka kwa chipani cha MCP pofuna kukhwimitsa mfundo zake za ufulu wa demokalase ndi ulamuliro wabwino; poonetsetsa kuti ntchitoyi ikuyendetsedwa ndi katswiri komanso munthu odziwa, ndiodalirika pantchito yoyimila anthu pamilandu komanso pankhani zamalamulo.