Wokondedwa Mkozi,

Ndakhudzidwa kwambili pa zimene atulankhani ena akuchita mdziko muno zimene zikhoza kutiwonongela mtendele umene dziko lino timakhala nawo.

Nthawi ino yachisankho ndiyovuta kwambili, anthu akhoza kumenyana kapena kuphana kumene ngati atulankhani sasamala m’magwiridwe awo antchito.

Atulankhani amenewa akumalemba mphekesera zakuti president wadziko lino Mayi Joyce Banda akufuna kubera zisankho za pa May pano. Akumangolemba izi alibe ndi umboni omwe. Izi zikhoza kubweletsa Phungwepungwe m’dziko muno ngati sitisamala. Ngati mwapeza umboni, bwanji osakasuma ku bungwe loyendetsa zisankho?

Asatinamize atulankhani amenewa kuti akuchita izi chifukwa chokonda dziko lawo, ayi, akuchita izi chifukwa chokonda mimba zawo. Iwowa analembedwa ntchito ndi azitsogoleri otsutsa m’boma kuti awathandize campaign ndi cholinga chakuti adzawaganizire m’maundindo osiyanasiyana ngati chipani chawo chingadzapambane.

Izi sizolokwika koma kumagwiritsa ntchito dzina la utulankhani kufuna kukwanilitsa zolinga zokomela iwo eni sizinthu zabwino. Tikudziwa atulankhani ena monga Brian Banda kuti amachita zinthu mowonjeza muyeso akudziwa kuti zinthu zikasintha akhala kufupi ndi kuphika.

Chimene ndikunena ine ndi chakuti sizowona kuti Asokoneze mtendele wadziko lino chifukwa cha zolinga zawo.

Dziko ili likadzakhala pa moto anthu ena ndikuluza miyoyo yawo chifukwa cha ma bodza anu amene mumati ma propaganda pa chingelezi, Mwazi wa anthu okufawo udzakhala m’manja mwanu.

Mukuona ngati anthu kuphedwa monga m’mene anaphedwela Robert Chasowa komanso anthu 20 pa 20th July 2011 paja munthu nkukhala ndi mtendele mumtima?

Tiyeni tilikonde dziko lanthu!

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

The Maravi Post has over one billion views since its inception in December of 2009. Viewed in over 100 countries Follow US: Twitter @maravipost Facebook Page : maravipost Instagram: maravipost