LILONGWE (MaraPost)—Peter Mutharika amene walumbilitsidwa mtsiku la lero ngati president wadziko la Malawi wapempha anthu onse mdziko muno kuti agwirane manja kuti apititse patsogolo chitukuko chadziko lino.
Polankhula pamsonkhano wa Atolankhani umene wamalizika posachedwa kunyumba kwake ku Nyambdwe mu mzinda wa Blantyre, umene umayendetsedwa ndi bambo Bright Malopa, Mutharika wati Nthawi yakwana kuti dziko la Malawi lipite patsogolo komanso kuti bata ndi mtendele zipite patsogolo.
Iwo ati alengeza cabinet yawo posachedwa. Iwo anenetsa kuti sakhulupilira kuchotsa anthu zintchito boma likasintha monga zakhalalilamu.
Pokambapo nkhani za kubedwa kwa ndalama za boma, iwo ati awonetsetsa kuti Chilungumo chidziwike malingana ndi Malamulo adziko.
Mutharika wakhala President wachikhumi wadziko lino. Pakadali pano , Mtsogoleri wopuma wadziko lino Joyce Banda komanso m’modzi mwa amene anapikisana nawo pa u president bambo Atupele Muluzi ayamakira a Mutharika kamba kowina kwawo.