A maumau osasamba amene akhala akugaza anthu osalakwa m’boma la Mulanje kamba kowaganizira kuti akuziwapo kanthu pa nkhambakamwa zomwe zili mkamwamkamwa kunena kuti anthu akuyamwidya ndikupopedwa magazi apangitsa kuti ziko la Amerika liuze anthu ake kuti asapite ku Mulanje pakadali pano.

Izizi ndizinthu zochititsa manyazi kwa dziko lonse ndiponso zotayitsa nthawi komanso kuluzitsa ndalama kwa anthu a bizimezi omwe amadalira anthu okaona chilengedwe m’bomalo.

Mchikalata chomwe chatulutsidwa sabata yathayi, dziko la Amerika lati ngakhale apolisi akuti palibe akuyamwidwa magazi mbuli zina kufupi ndi ku Limbuli sizikusiyabe kupanga za umbuli zawo zowononga katundu, kugenda, kuotcha ndi kupha anthu omwe anamizilidwa kuti ndi opopa magazi.

Werengani chikalatacho apa

Tili ndi chikhulupiliro kuti anthu a ku Mulanje sali ngati zigawenga za ku Ndirande ndipo kuti ali ndi mitima yokongala ngati mapiri, nkhaka, nanazi ndi misinje ya ku Mulanjeko ndipo kuti ayesesa kuti athane ndi zigawenga zomwe zikukanika kupeza akazi ndiponso zilibe ndalama zomwe zikupangitsa kuti zizichitira nsanje anthu akamakwera magalimoto ndikuoneka ngati ali ndi ndalama.

Asiyeni apolisi agwire ntchito yawo, ngati ena akusowa ndalama apite ku ma esiteti ali nawo pafupi azikatola magede ndikuthyola tiyi chifukwa zauchifwamba zikuononga myoyo ya anthu osalakwa.

NBS Bank Your Caring Bank