Wolemba: Falles Kamanga
Pomwe misankhano yosatha ikumakhazitsidwa pofuna kudabwitsa anthu ,Chilima wadzaso ndi mfundo zake pofunitsitsa kukopa anthu;koma iye akhala bwanji osakhutitsidwa?Chifukwa ndichokuti anthu ambiri akuzindikira kuti Iye si yankho kumavuto omwe dziko la Malawi likukumana nalo
Tiyeni tione lonjezo lake lomwe anati azakhazikitsa ntchito 1 Million mu chaka chimodzi.Atafusidwa za nkhaniyi ndi Zeinab Bedawi ,Mtolankhani wa BBC mu program ya Hard Talk iye anakanika kupereka tsatanetsatane wa momwe azakwanilitsie izi mu dziko lovuta nkhani ya zachuma ngati Malawi
Malingana ndi Happy Chirwa,Katswiri pa nkhani zosiyanasiyana anayankhula pa kanema wa MBC kuti Company yaikulu imakwanitsa kulemba ntchito anthu 4000,mwachitsanzo kampani ya Illovo ndipo iye anati zitengera Malawi kukhala ndi company 250 zokhala ngati Illovo kuti Chilima azakwanise kulemba anthu 1 million ntchito ndipo mpomwe akuti apa mpomwe pakubwera bodza la mkuluyi
Chirwa akutsutsanaso ndi ganizo la Chilima ponena kuti ngakhale chilima atakhazikitsa ngongole ya 40 billion sangakwanitsebe kukhazikitsa ntchito 1 million. Iye wati anthu 200000 atha kulemba anthu 5 zomwe ndizosatheka kwa munthu yemwe akupanga business ndi kapitolo la 200000 kwacha kulemba anthuwa
Chinaso ndichakuti Chilima samatsutsika ponena zinthu zoti ndizabodza .
Ndi ndani yemwe amasamala kumva mfundo zogwirika pomwe wina akungolonjeza zinthu zaulele popanda cholowa chilichose?Sizodabwitsa kumva zoti Chilima akuyankhula zinthu zongopeka?
Zikuonetsa kuti Chilima akuchita zinthu mokakamizidwa popanda mfundo zomutsogolera .Zachidziwikire kuti pakadali pano khumbo lake ndikukhala mtsogoleri wa dziko basi .Komatu iye akuyenera kutiuza zinthu zogwirika
Chilima mukuganiza kwake koperewera akuona ngati kulonjeza zinthu zomwe sizikufunika changu ndi zomwe a Malawi angakonde ndipo nthawi zambiri Chilima wakhala akunena zinthu zomwe ena ananena kale ngati kuvomereza Chamba komanso nkhani za grewm belt .
Izi zikuonetsa umbuli wake onse ndipo zikusonyeza kuti iye alibe mfundo zatsogolo koma mfundo zomwe zili zopanda phindu kwa Amalawi
Pali kukambirana pa ganizo lake lofuna kuvomerezq kuchotsa pakati pochepetsa imfa za ubereki zomwe mpingo wa Katolika sumagwirizana nazo.Iye watonso atha kunena pagulu zachuma chake poonetsa chilungamo ndinso kuulura anthu okhudzidwa pa nkhani zakatangale pothetsa mchitidwewu..Koma nanga kodi anthu omwe azaulurridwewo azamusiya naye potengera khalidwe lake mzaka za m’mbuyomu??
Tili ndi chikhulupiliro kuti lonjezo lake lina lizakhala lochotsa msonkho pa mowa potengera nkhani zomwe zimamveka kuti naye ndi Chidakwa.
Chidziwitso: Maganizo muzolembedwa pa nkhaniyi siza Maravi Post kapena Mkozi wake koma za yemwemwe walemba nkhaniyi





