MCP Veep Sidik Mia  agwedeza ndikubooleza  Mangochi Nkungulu

MANGOCHI-(MaraviPost)-Chikhwimbi cha mwana wa munthu ku Mangochi-Nkungulu chinakhamukira pa bwalo la sukulu ya pulaimale ya Chapola kudzaona wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Kongeresi, Muhammed Sidik Mia pa chimsonkhano chokopa anthu kuti adzavotere chipanichi chomwe anapangitsa Lachiwiri.

 

Poyankhula ku humankind chinasonkhana, Mia anatsimikidzira anthu a m’derali komanso m’boma lonse la Mangochi kuti konse-konse komwe iye waponda, zachita kuonetseratu kuti chipani cha Kongeresi ndi chomwe chipambane chisankho cha patatu chomwe chikhalepo pa 21 Meyi mwedzi wamawa.

 

Mia yemwenso adzaime ndi mtsogoleri wa MCP pa mpando wa Pulezidenti pa chisankhochi anati kasakaniza yemwe wachitika pa utsogoleri wa Kongeresi ndi yekhayo yemwe ali ndi kuthekera kolikonza dziko la Malawi kuti likhale lokomera anthu onse posayang’anira mtundu, ndale, chipembedzo komanso dela lomwe munthu akuchokera.

 

Pamfundoyi a Mia anatsindika kuti mtsogoleri wa chipanichi, Dr. Lazarus Chakwera ndi m’busa amene ali mtumiki wa Mulungu wa chipembedzo cha chi Khristu pamene wotsatira wake amene ali iye amene ndi mtsogoleri wa chipembedzo cha Chisilamu.

 

Potsindika, Mia anati nkosatheka kuti atsogoleri awiriwa omwe ngowopa Chauta adzatsogolere Amalawi mophotchola monga momwe amachitira atsogoleri ena omwe saladira kwenikweni za Chauta.

 

Powonjezera apo, a Mia anati mgwirizano womwe Kongeresi yachita ndi chipani cha Peoples komanso chipani cha Freedom ndi zaonetseratu kuti nthawi yakwana yoti utsogoleri wa dziko lino upite mmanja mwa Kongeresi.

 

Pokambapo pa zomwe Kongeresi idzichite ikalowa m’boma, a Mia anati boma la chipanichi lidzatukula umoyo wa anthu m’magawo a za ulimi, za umoyo, maphunziro komanso potukula achinyamata ndi amayi.

 

Pongotchulapo, a Mia anati boma la MCP lidzaonetsetsa kuti ophunzira sakuphunziranso pansi pa mtengo monga zilili panopa.

 

Ku mbali ya za umoyo, iwo anati, kongeresi idzaonetsetsa kuti pali zipatala zokwanira m’madela onse a m’dziko muno komanso kuti ulemu wa amayi oyembekezera udzabwelera monga mwakale pamene azamba achizimayi okha ndi omwe adzidzathandiza amayi pa nkhani za ubereki maka nthawi yoti mayi woyembekezera achile ikafika.

 

Pachinsonkhanochi panalinso akulu-akulu ena a Kongeresi ochokera m’komiti yaikulu ya chipanichi monga, a Lawrence Malemia, a Ramsey Khan,  a Edgar Chipalanjira komanso yemwe adzaimire chipanichi pa mpando wa phungu, a Noel Makawa.

 

Potengera m’gwirizano wake ndi chipani cha Peoples chomwe mtsogoleri wake ndi Mayi Joyce Banda omwenso ndi mtsogoleri wopuma wa dziko lino, pamsonkhanowu panalinso akulu-akulu komanso ma sapota a chipanichi omwe anatsogozedwa ndi Provincial Chairman wa m’chigawo cha kum’mawa, a Muhammed Matola.

 

Mu kuyankhula kwawo, a Matola anapempha mamembala komanso anthu onse omwe anatsatira chipani cha PP kuti adzavotere Pulezedenti komanso phungu wa Kongeresi pa chisankho chomwe chikubwerachi.

The Maravi Post has over one billion views since its inception in December of 2009. Viewed in over 100 countries Follow US: Twitter @maravipost Facebook Page : maravipost Instagram: maravipost