Donated cow

Wolemba Mtolankhani wathu

CHIKWAWA-(MaraviPost)-Wachiwiri kwa nduna ya zamalo, Mayi Abida Mia yemwenso ndi phungu woimila dera la Chikwawa Nkombezi wapereka nyama ya ng’ombe kwa achipatala omwe ali pa kalikiliki kuthandiza odwala matenda a Covid 19 pa chipatala cha gulupu mu mzinda wa Blantyre.

Wolemekezeka Mayi Mia apereka nyamayi kudzera ku banja la Bambo ndi Mayi Kulemeka omwe akukhala mu mzinda wa Blantyre ndipo adayambitsa ntchito zachifundo zomapereka chakudya chaulere kwa achipatala omwe akuthandiza odwala matenda a Covid 19 pachipatala cha gulupu chomwenso chimatchuka ndi dzina loti Queen Elizabeth Central Hospital.

Poyankhula ndi mtolankhani wathu, a Mia omwenso amadziwika bwino ndi ntchito zachifundo, afotokoza kuti, chidali cholinga cha malemu amuna awo, a Muhammed Sidik Mia kuti achipatala omwe usana ndi usiku akugwira ntchito yopambana yolimbana ndi mliri wa Covid 19 ayambe kuwapatsa nyama yoti adzipanga ndiwo pa nthawi yomwe akugwira ntchito.

Iwo adati malemu Mia adanena kuti adali okonzeka kumapereka nyama kwa achipatalawo kufikira pomwe Covid 19 idzagonjetsedwe.

Mwa ichi, Mayi Mia anati iwo akhala akupereka nyama kwa achipatalawo pokwaniritsa zomwe malemu Sidik Mia adali okonzeka kudzikwaniritsa.

Malemu Mia omwe adali nduna ya boma komanso wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha kongeresi, adamwalira pa chipatala cha gulupu sabata ziwiri zapitazo atadwala matenda a Covid 19.

Mwambo wolandira nyamayo unachitika m’mawa wa Lolemba pa kampani ya S & A Cold Storage mu mzinda womwewo wa Blantyre pamene Bambo Andrew Kulemeka pamodzi ndi akazi awo, Mayi Della Kulemeka analandira nkhunzi ya mtundu wa Brahman yolemera makilogalamu 743 ndipo pambuyo poipha ndi kuikonza ilemera makilogalamu 400.

Malinga ndi a Della Kulemeka omwe akutsogolera ntchito yophikira achipatala chakudya chaulere, anthu akuyenera kutengera chitsanzo cha ‘mlerakhungwa’ chomwe Mayi Mia awonetsa popereka nyama kwa anthu omwe akugwira ntchito yotamandika.

Iwo anathokoza wachiwiri kwa ndunayu chifukwa cholonjeza kuti adzipereka nyama kwa achipatalawo kufikira mtsogolo muno pomwe Covid 19 idzasiye kukhala chiopsezo.

Sabata yapitayo, olemekezeka Mayi Mia adaperekanso mpunga wolemera makilogalamu 300 kwa achipatalawo kudzera ku banja lomweli la Bambo ndi Mayi Kulemeka.

Banja la a Kulemeka lidayamba kugwira ntchito zachifundo zomaphika chakudya nkuchipereka mwaulere kwa achipatala omwe akulimbana ndi Covid 19 sabata yapitapiyo.

Iwo adayamba ntchitoyi ndi ndalama za mthumba mwawo zokwana I miliyoni kwacha.

Kudzera mwa anthu akufuna kwabwino, banja la a Kulemeka likumasonkhetsa ndalama zomwe akugulira chakudya komanso kulipira akatswiri odziwa kuphika omwe amawapempha kuti akonze chakudyacho pofuna kuti chidzikhala cholongosoka.

The Maravi Post has over one billion views since its inception in December of 2009. Viewed in over 100 countries Follow US: Twitter @maravipost Facebook Page : maravipost Instagram: maravipost    
NBS Bank Your Caring Bank