LILONGWE (MaraviPost) — Pulezidenti wa dziko lino a Peter Mutharika sayankhaso mlandu wawo womwe ankawaganizira kuti ankafuna kulanda boma, atangomwalira mchimwene wawo Bingu wa Mutharika m’chaka cha 2012.

Malingana ndi a Bruno Kalemba, mkulu wozenga milandu ya boma, gawo 77 la malamulo a dziko la Malawi, limaletsa kuzenga mlandu pulezidenti.

Mlanduwu wathetsedwa a Mutharika atakhala masabata osapyola anayi chipambanireni chisankho cha patatu cha pa 20 Meyi.

Ena mwa oganiziridwa mu mlanduwu adali Goodall Gondwe omwe awasankha kukhala nduna ya za chuma, Patricia Kaliati, Bright Msaka, Symon Vuwa Kaunda, Henry Mussa, Nicholas Dausi omwe wasankha kukhala woyan’anira za ukazitape komanso Kondwani Nankhumwa.

Malingana ndi ogwira ntchito ku unduna wa za malamulo omwe sanafune kutchulidwa chifukwa choti a Mutharika, omwe anali woganiziridwa wamkulu m mlanduwu, sangazengedwenso zikuyenera kukhalanso choncho kwa ena.

The Maravi Post has over one billion views since its inception in December of 2009. Viewed in over 100 countries Follow US: Twitter @maravipost Facebook Page : maravipost Instagram: maravipost