Wolemba Kondanani Chilimunthaka
LILONGWE-(MaraviPost)-Dziko la Malawi lachisanu pa 6 Juni 2025 linali ndi mwayi owona mmodzi wa aphunzitsi omwe adapanga nawo Mtsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera kukhala ndi ukadaulo wamaphunziro komanso kukhala chomwe iye ali lero.
Mwambo omwe Pulezidenti Chakwera anakonza kunyumba ya chifumu ya Kamuzu mu mzinda wa Lilongwe, ozindikira ntchito yapamwamba yomwe aphunzitsi amagwira, unabweretsanso poyera bambo Michael Chatsunda Banda, omwe akhale akukwanitsa zaka 93 zakubadwa chaka chino, ndipo adasula mtsogoleri wa dziko lino pa sukulu ya pulayimale ya Kaning’a ku Nambuma, m’boma la Dowa.
Mukanema yemwe anawonetsedwa pa mwambowu, a Chatsunda anati a Chakwera anali mnyamata odzipereka komanso osunga mwambo, zomwe zinapangitsa kuti azichita bwino mkalasi. Iwo anatsindikanso mkanemayu kufunika koti aphunzitsi azikonda ntchito yawo.
“Mau kwa aphunzitsi azanga omwe akugwira ntchitoyi, azigwira modzipereka ndi mokhulupilika posatengera ndalama zomwe amalandira pakutha pa mwezi, chifukwa iwo ali ngati nyundo yosulira makasu kuti akalime mphanje” Anatero a Chatsunda Banda mkanemayu.
Naye Mtsogoleri wa dziko lino mmau ake anati aphunzitsi ndi ofunika kwambiri pa chitukuko cha dziko, ndipo kuti boma lake lipitilira kuyika zofunikira pofuna kutukula luso la aphunzitsi pambali pokhala ndi sukulu zapamwamba zosula aphunzitsiwa monga Domasi ndi Nalukule.
Mwambowu omwe unadziwika ndi dzina loti “Chakwera Classroom Heroes” pa chingerezi, ndi oyamba kuchitika mdziko muno, ndipo aphunzitsi omwe anasankhidwa alandira mendulo za ulemu kuchokera kwa Mtsogoleri wa dziko linoyu.



