Mafumu a ku Chamalaza mumzinda wa Mzuzu awalangiza kuti asafunse dipo kapena ndalama pochitira  umboni  munthu wa chilendo kapena wa mmudzi mwawo  kuti alembetse mukaundula wa za chisankho chifukwa kutero ndi mulandu ndipo akapezeka azamangidwa.

Mkulu woyang’anira zophunzitsa wanthu pa nkhani za chisankho mumzindawu mayi Naomi Gondwe NyaMNyirenda  ndiye adanena izi lachitatu pamemne amachezera azimayi, mafumu, zinduna, anthu a matchalichi osiyanasiyana ndinso akuluakulu a zipani zosiyanasiyana pa sukulu ya Chamalaza .

Mayi Gondwe NyamNyirenda adati  mfumu kuwunikira anthu ache pa zitukuko zosiyanasiyana zochitika mmudzi mwache ndi ntchito yache kuyikira umboni ndipo sayenera kufupidwa pokhetsa thukuta pantchitoyi.

Iwo ati mfumu yachoncho ilibe chikondi ndi anthu ache ndipo ndiyachinyengo yoyenera kumangidwa.

Mayiyu wanena izi malingana kuti dziko la Malawi chaka cha mawa pa May 20, lizakhara ndizisankho zapatatu kwa nthawi yoyamba muzakazambirimbiri pomwe nzika za dziko lino zizasankha phungu, mlangizi wadera ndinso mkulu wadziko(pulezidenti).

Koma izi zisadachitike, munthu ayenera kulembetsa kaye kuti azathe kusankha bwino atsogoleriwa.

Pamene kumadera ena kalemberayu adayamba kale,mumzimdawu, kulembetsa kudzachitika pa Decembala 5 ndipo kuzatha pa Decembala 18 2013.

Mayi Nyamnyirendawa ati  kuti munthu ulembetse bwino payenera kukhara chiphatso monga choyendetsera galimoto, choyendera kunja kapena chikalata chochokera kwamfumu kuyikira umboni kuti ndiwedi nzika ya Malawi.

Mayi Nyamnyirenda ati otsalembetsa asemphana ndi zabwino zambiri chifukwa chiphatso choponyera voti ndichabwino kwambiri  pazitukuko zambiri zomwe munthu nkupezapo phindu. Iwo adati ndiphatso choponyera voti munthu ungathe kutengera ndalama ku banki, ndizabwino zotero.

Polankhulaposo pa nkhani yolembetsa yomweyo, mayi Rabecca Hara Chisanya omwe ndinamandwa pophunzitsa nkhani za zisankho adati  kulembetsa kawiri kuti chipani  chomwe  amachikonda chipambane kwambiri ndi mlandu waukulu woti munthu kumangidwa.

Iwo ati ngati chithunzi chomwe wina wajambulitsa patsikulo sichidamusangalatse ndi bwino kujambulanso kachiwiri kusiyana ndi kulembetsa kawiri.

Komanso anthu akuChamalaza awuzidwa kuti asazavale Malaya a mtundu wa chipani chomwe iwo amachikonda panthawi yakalemberayi chifukwa kutero kuli ngati ukukopa wanthu kapena kuzetsa ziwawa pamalo a boma.

Anthuwa awuzidwanso kuti apite akalembetse mwaunyinji wawo tsiku likafika chifukwa kulibe kuonjezera matsiku pazifukwa zochedwera  dala.

Mmalo mwawo, mfumu Galang’ombe ya kuchamalaza yathokoza bungwe lachisankholi chifukwa cha maphunzirowo eti awatsegulammaso.

The Maravi Post has over one billion views since its inception in December of 2009. Viewed in over 100 countries Follow US: Twitter @maravipost Facebook Page : maravipost Instagram: maravipost