MCHINJI-(MaraviPost)-Mfumu yayikulu Mavwere ya Boma la Mchinji yati Pulezidenti Dr. Lazarus McCarthy Chakwera sakuchoka pa mpando.
Gogo Mavwere yanena izi lachiwiri pa Waliranji Trading Centre M’boma la Mchinji pa misonkhano yoyimayima yomwe Pulezidenti Chakwera akupangitsa m’bomalo.
M’mawu ake, a Mavwere anati anthu a m’dera lake adzavotera Chakwera ndi cholinga chakuti chitukuko chomwe chayambika kale chipitilire kufalikila dziko lonse la Malawi.
A Mavwere anathokozanso Pulezidenti Chakwera chifukwa cha mswahala omwe mafumu ambiri a m’delaro akulandila.
“Ma voti tapukuta kale . Ndikunenetsa kuti kumene kuja (nyumba ya chifumu) simuchoka bwana. Zonse takonza kale kuti zitukuko zayambikazi zipitilile,” inatero Mfumu Mavwere.
Phungu wa Nyumba ya Malamulo a Agness Nkusa Nkhoma anati anthu a m’dera lake adzavotera Pulezidenti Chakwera.
“Bwana mudzigona ndi make khutu yemwe. Mavoti kuno tikupatsani migolo migolo,” anatero Mai Nkusa Nkhoma.
Mlembi wankulu wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP) a Richard Chimwendo Banda anapempha anthuwo kuti adzatulike mwa unyinji pa 16 Sepitembala kukavotera Chakwera.





