Nyumba ya wachiwiri kwa pulezidenti waziko lino Dr Saulos Chilima yomwe ilim’mzinda wa Lilongwe makamaka ku area 12 inasanduka bwalo lomenyera masewero ankhonya kapena judo pakati pa akuluakulu a chipani cha UTM omwe amakanganiralana mawudindo.
Izi zilichomwechi kambaka kawusogoleri osakhwima wa Pulezidenti wa chipani cha UTM Dr Chilima omwenso wapangisa kuti chipanichi chisokonekere.
Malingana ndi achitetezo akunyumba ya Chilima omwe anakanitsitsa kuwatchula mayina awo, a Labal Omar ndi a Newton Kambala yemwenso ndi Pulezidenti wa chipani cha UTP ndiomwe anayambitsa kuponyerana zibakira patsikuli kupatula kuopyeza kuthetsa m’gwiridzano wawo ndi chipani cha UTM.
Kafukufuku yemwe mtolankhaniyi wapanga wawonetsa kuti chipani cha UTM inatsekapakamwa nyumba zowulutsa mawu zina zamziko muno kuti zisawulutse nkhaniyi koma zofowoka komanso zoipa za chipani cha Malawi Congress Party (MCP).
Mtolankhaniyu wapezanso kuti chipani cha UTM chinapereka ndalama zokwana K200, 000 kwa atolonkhani a nyuzipepala ya Nationa, Times komanso Zodiak omwe amawona momwe a Anitta Kalinde anatukanidwira pamsonkhano wa komiti yaikulu ya chipani cha UTM chinapangitsa.
A Kalinde malingana ndimalipoti anatukwanidwa, kuwopyezedwa kuti awagwirira komanso kuthamangisidwa patsikuli ndi zigawenga za Kambala ndi aMasangwi.
Ndewu yapakati pa a Omar ndi aKambala idabuka kamba koti aOrmar amamenyera nkhondo a Patricia Kaliyati [mlembi wa mkulu wa UTM] kuti azikhala ndiowasatira ambiri.
A Ormar anawulura poyera kuti a Kambala akusunga mpeni kumphatsa makamaka pokhala ndimapulani ogwetsa a Chilima pamupando wa upulezidenti wa chipani cha UTM kumsonkhano wawo waukulu omwe ukhadzakhala pa 17 December chakachino.
Gulu la aKambala lomwe kulinso a Kalinde ndi Manganya linatukwana a Ormar powatchula kuti “m’mwenye opanda anthu, osokonedza komanso opanda ndalama.”
“A Chilima omwe anali atalezereratu panthawiyi anangochokapo kusiya mbali ziwirizi zikutibulana monga achitira Jet Li. Ndipo zinatengera achitetezo a Dr Chilima kuleretsa ndewuyi ngakhale amapitiliza kutukwanidzana,” anatero m’modzi mwa akulu achipani cha UTM omwenso anati palikagulu kena komwe kakumemedza mamembala a UTM kujoyina chipani cha Joyce Banda cha Peoples Party (PP).
Mchipani cha UTM muli magulu atatu ndipo pa akuluakuku amagulu atatuwa a Kiyati ndiomwe alindimphamvu kwambiri kuposa a Masangwi omwe akulimbitsidwa Ndi governor wangosankhidwa kumene wa chigawo chakumwera a Mikaya.
Malingana ndimalipoti, Kaliyati ndiyemwe akuyembekedzera kukhala wachiwiri kwa chilima pachitsankho chikubwerachi kambakoti ndiotchuka kuposa a Michael Usi komanso a Lovemore Munlo makamaka kwa anthu a chilomwe komwe chipanichi chikufunitsitsa kusankha osatila a Chilima.
Kalinde ndiyemwe akumemeza anthu kujoyina chipani cha PP ponenakuti UTM ilibetsogolo.
Mbali ya a Masangwi ilibiletu tsogolo kambakoti udindowake wapam’mpando wa mkulu wa chioanichi anawuthesa.
Poyankhapo pankhayi, a Ormar anadzudzula anthu omwe anawulura nkhaniyi ponenakuti inaliyamunyumba yawo pamene a Kalinde anawopyeza kuthana ndigulu lomwe linatengapo mbali pomutukwana.
Mneneri wachipanichi a Chidanti Malunga sadayankhekanthu zankhaniyi kambakoti lamya yawo yam’manja simagwiri.





