Politics

Mwini Galu wadziwika pachisokonezo ku DPP

1 Min Read

LILONGWE-(MaraviPost)-Chipani cha Malawi Congress Party (MCP) chadzudzula chipani chachikulu chotsutsa boma cha Democratic Progressive Party (DPP) ati kaamba kochotsa ma membala ake ena mu chipanicho.

Mu kalata yomwe MCP yatulutsa yati zomwe yachita DPP ndi zotsutsana ndi mfundo za demokalase zomwe zimalimbikisa kulolelana ngakhale mkati mwa chipani.

Mu kalata yomwe wasainira ndi mneneri wa MCP a Ezekiel Ching’oma, chapanichi chati ku mbali yake chipitiriza kulemekeza mfundo za demokalase zomwe mtsogoleri wa chipanicho komanso dziko a Lazarus Chakwera amalimbikisanso.

Chipani cha DPP dzulo chinalengeza kuti chachotsa mu chipanicho a Kondwani Nankhumwa, a Grelzeder Jeffrey ndi akuluakulu ena, ndipo ayimikidwa kaye kukhala ma membala a chipanichi kwa miyezi isanu ndi inayi.

A Nankhumwa, omwe ndi mtsogoleri wa otsutsa boma ku Nyumba ya Malamulo, akhala akutengera chipanichi ku bwalo la milandu pa zifukwa zosiyanasiyana.

Maravi Post Reporter

Op-Ed Columnists, Opinion contributors and one submissions are posted under this Author. In our By-lines we still give Credit to the right Author. However we stand by all reports posted by Maravi Post Reporter.