Opinion

Mfiti simveledwa chisoni

3 Min Read
Message to Bullets and Wanderers supporters: this is what people in Mzimba got when Peter Mutharika promised them a University

Wolemba Patseni Mauka

 

Munthu akagwidwa ufiti amamvetsa chisoni. Kangapo konse, ndaona mfiti zili mbulanda pa denga la nyumba yotsilika. Zimakhala jenkha kubisa maliseche zitawelamira pansi ndi manyazi. Mfitizi zimakhala kuti zimapita kotamba ndipo njira ya ndege yawo kapena kuti flight path mu chingerezi, inadutsa nyumba yotsilika. Nthawi zina zimakhala kuti zimapita kukatamba nyumba yomwe ndi yotsilika.

 

Zifukwa zimene ndege zodziwika bwino zimagwera, sizosiyana ndi zifukwa zomwe ndege za ufiti zimagwera. Nthawi zambiri ndege za zitsulo zimagwa chifukwa cha nyengo yoyipa, kulakwitsa mayendetsedwe, kulakwitsa kukonza ndege ndi zina zambiri. Oyendetsa ndege za zitsulo amayenera kufufuza za nyengo asananyamuke ulendo kuopetsa ngozi. Ndikhulupira kuti oyendetsa ndege za ufiti ameyeneranso kufufuza misewu yabwino yopanda nyumba kapena manda otsilika. Ndege za zitsulo zikagwa timamva chisoni. Koma ndege za ufiti monga malichero ndi nsupa zina zikagwa timakondwa ndikuthamanga kukaona, kuseka ndikunyogodola mfiti.

 

Ufiti ulipo mitundu yambiri. Ufiti sikutamba kokha. Ufiti sinyanga zokha. Zochita za munthu zimatha kuonetsa kuti uyu ndi mfiti. Munthu wopanda nyanga koma woyipa ngati satana timamutcha mfiti. Agogo anga anandiuza kuti pamudzi kapena pabanja pakakhala anthu wosaphunzira ambiri, pamakhala ufiti.

 

Pabanja pakakhala munthu mmodzi wophunzira, wa ntchito yabwino, ena onse amangoyembekezera chithandizo kuchoka kwa iye. Amafuna kuwagulira nsapato, miyado, zakudya and zina zambiri. Ena mpakana amafuna awapangire ukwati, kuwalipilira chili chonse cha pa ukwati, ndi suti yomwe kuwagulira. Akakwatira amafunanso kumawalipilira nyumba yokhala ndi ‘kuwabwereka ndalama zogulira zakudya’. Ndalama zobwelekazonso sabweza. Umenewu ndi ufiti wawukulu woposa wa nyanga.

 

Ku ndalenso kuli ufiti. A ndale ena amadziwa kuliswa bodza lankukhuniza. Bodza lawo limachita kuoneka ngati anapita kusukulu ya ukachenjede kukaphunzira kunama mopanda manyazi. Chisankho cha chaka cha 2014, Pulezidenti wolephera, Pitala Mutharika, anatiuza kuti akadzangopambana chisankho, adzakwera ndege ya helokopita ndikupita ku nsanje kukatsekulira doko la sitima za pa madzi. Koma pano zaka zisanu zapita, akuluwa sanakwanitse lonjezo lawo.

 

Anthu aku Nsanje, omwenso analonjezedwa mzinda waukulu, angodikirabe mpaka lero. Powona kuti chimwala chimene chimayenera kukhala doko chingokhala nkuvumbidwa mvula chaka chili chonse, anthu a ku Nsanje, akugwiritsa ntchito malowa ngati pomangira ukwati, kumwa thobwa, kudya, ndi kuponya dansi. Zoseketsa komabe zomvetsa chisoni kwambiri.

 

Bambo Mutharika adalonjezanso kuti azamanga sukulu za ukachenjede zisanu mu boma la Mzimba, Mangochi, Nkhotakota, Karonga ndi Nsanje. Achinyamata amene anali folomu 1 mu chaka cha 2014 anasangalala kuti akamadzafika folumu 4, kudzakhala kuli ma masukulu a ukachenyede owonjezera asanu. Zachisoni kuti zaka zisanu zatha ndipo Mutharika walephera kukwanitsa malonjezo ake.

 

Ngakhale walephera kukwanilitsa malonjezo ndatchulawa ndi ena ochuluka, Mutharika walonjezanso ma bwalo amasewera a mpira wa ‘mapazi’ awiri kwa ma timu a mpira a Bullets ndi Wanderers. Mutharika walonjezanso msika watsopano ku Zingwangwa. Kodi umenewu siufiti? Uthakati umanenedwa uja siimenewu? Cholonjezera zinthu zokuti akukanika kukwanitsa ndi chani?

 

Amalawi anzanga, tisavotere munthu pomvera chisoni. Inde amati osasunza nkhalamba kapena azigogo athu koma nkhalamba iyi ikuseweletsa tsogolo la Malawi. Nkhalamba ya bodza lopanda nalo manyazi, yakatangale ndi yogwilitsa ntchito achinyamata kutema ndi ndikuvulaza anthu ichoke!

 

Patseni Mauka

Patseni Mauka is a Contributor at The Maravi Post and a Political Commentator in Malawi. His hard hitting Political views have a strong following on Social Media