BLANTYRE-(MaraviPost)-Mafumu ena amtundu wa Alhomwe m’maboma a Thyolo, Mulanje, Phalombe, Chiradzulu, Zomba ndi Blantyre adandaula kuti kukwezedwa kwa Senior Chief Kaduya ya m’boma la Phalombe, dzulo Lachinayi pa 18 January 2024, kukhala mfumu yaikulu (Paramount Chief) ya Alhomwe ndichisokonezo chachikulu kaamba koti a Kaduya ndi m’Mang’anja, osati mu Lhomwe.
President Lazarus Chakwera ndiye adatsogolera mwambo wokweza Senior Chief Kaduya kukhala Paramount wa Alhomwe.
Mafumuwa apereka dandauloli pa nkumano wao, womwe anatsogolera ndi Senior Chief Ndalama a m’boma la Thyolo ndi Senior Chief Nkhulambe a m’boma la Phalombe, ku Mtundawosema (ku likulu la malemu Paramount Chief Ngolongoliwa) m’boma la Thyolo.
Mafumuwa apereka nkhawa zawo pamsokhano wa atolankhani lero ku Thyolo.
Iwo atsimikiza kuti achita chotheka kuti boma limve pempho lawo kuti yemwe akuyenera kulowa m’malo mwa malemu Paramount Chief Ngolongoliwa akuyenera kukhala mu Lhomwe, osati wa mtundu wina.
Mafumuwa atinso ndondomeko yoyenera posankha mfumuyi sinatsatidwe komanso board ya Mlakho wa Alhomwe siinalumikizane nawo padongosololi.
Source: Nation online





