Politics

“Sitimadana ndi boma lanu”-Mavenda a mumzinda wa Mzuzu atsimikizira Chakwera

1 Min Read

MZUZU-(MaraviPost)-Ochita malonda osiyanasiyana mu mmisika ya mu mzinda wa Mzuzu ati iwo sakudana ndi utsogoleri wa Pulezidenti Lazarus Chakwera, ndipo ati iwo ndiwodzipereka kwathunthu kuthandiza boma lake kutukula Malawi.

Ochita malondawa alankhula izi lachiwiri pa 4 March 2025, pomwe anakumana ndi Mtsogoleri wa dziko lino Chakwera kunyumba yaboma ya Mzuzu State Lodge.

Polankhula kudzera mwa mtsogoleri wawo, Gerald Maulana, ochita malondawa ati atamva kuti Mtsogoleri wa dziko wawayitana kuti akakambirane zokhudza umoyo wawo, iwo anachiwona cha nzeru kuti ayimitse chikonzero chawo chofuna kuchita ziwonetsero pofuna kupereka nkhawa zawo kwa Mtsogoleriyu, ndipo kuti mmalo mwake akumane naye ndikutula nkhawa zawozi.

“Sitikudana ndi utsogoleri wanu, ndipo mukationa tikulira, muzidziwa kuti tili ndi madando ofuna inu mulowererepo monga tate wathu. Ndiye titamva kuti inu mwavomera kukumana nafe lero, panalibenso chifukwa choti ife tikayendere pa nsewu kukatula nkhawa zathu kukhonsolo, mmalo modzapereka kwa inu.

“Inu ndinu Mtsogoleri owopa Mulungu mchifukwa chake adakuyikani pampando panthawi yomwe dziko lathu likudutsa mmavuto ochuluka” anatsindika motero mtsogoleri wa ochita malondayu.

A Maula anathokonzanso Chakwera kamba kolowererapo nsanga madandaulo okhudza ochita malonda a Kaunjika mdziko muno, ponena kuti ichi mchitsimikizo kuti Mtsogoleriyu amayika zofuna za ochita malondawa pamtima pake.

Kumasanaku, Pulezidenti akuyembekezeka kutengera zomwe adankhula pomwe amatsekulira mkumano wa aphungu a nyumba ya Malamuro kwa achinyamata a chigawo cha Kumpoto pa mwambo omwe uchitikire ku Hotelo ya Grand Palace mu mzinda wa Mzuzu.


Discover more from The Maravi Post

Subscribe to get the latest posts sent to your email.

Discover more from The Maravi Post

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading