Politics

Kabambe ndi Nangula otumizidwa ndi Mulungu: aMalawi Musaphonye

4 Min Read

By Allan Ngumuya

Kuphonya Dr. Dalitso Kabambe pachisankho ichi, dziko la Malawi lidzola manyazi akulu pa maso Mulungu wolenga dzuwayo.

Pomwe dziko la Malawi lakonzekera kupita ku masankho apatatu ndi khamu la ofuna mpando wa utsogoleri wadziko, Dr Kabambe ndiyekhayo amene akupereka mfundo zogwirika; feteleza adzagulidwa K50,000 pathumba lolemera 50Kgs, osati mabodza enawa.

Ndipo payekhapayekha omwe akupikisana nawo pa mpando wa utsogoleri wadziko 17, akudziwa kuti Kabambe ndi michonya osati masewera ndipo sakufikapo pa iye.

Atsoleri okwana 17, akuvomereza mkati mwawo kuti aKabambe ndiye ali ndi mfundo komanso mayankha ogwirika pa mavuto a Malawi.

Dr. Dalitso Kabambe afikira boma lirilonse kugulitsa mfundo zawo kwa a Malawi, kufikira ngakhale madela a kumidzi kwenikweni.

Kusiyana kwina kwa a Kabambe ndi omwe akupikisana nawo ndi kuti a Kabambe akuwuza akufotokozera mavuto ndi yankho lake osati kungoyima mkumayankhula zosagwira mtima. Ndi mtsogoleri yekhayo amene ali ndi kuthekera, wagwira ntchito m’boma zaka 23 ndipo akudziwa bwino kayendetsedwe ka chuma komanso boma, komwe adawoneka kuti ndi olimbika pantchito, also komanso odzipereka kwathunthu.

Kunenetsa kuti a Kabambe awonetseratu kuti akhoza kuchita bwino kwambiri pa utsogoleri wadziko kusiyana ndi atsogoleli onse 6 omwe alamula dzikoli kumbuyoku.

Ukatswiri wa Dr. Kabambe ukubwera chifukwa chogwira ntchito m’boma kwa zaka 23 pansi pa atsogoleli okwana asanu ndi m’modzi, momga Dr. Bakili Muluzi kuyambira m’mchaka cha 1994, ndipo kenako anagwira ntchito yabwino ndi a Bingu wa Mutharika, Dr. Joyce Banda, Professor Arthur Peter Mutharika, ndi kuphatikizapo utsogoleri omwe ulipo pano.

A Kabambe ngakhale agwira ndi atsogoleli onsewa adawonetsa ukadawulo wawo ndi kukhwima pa nzeru makamaka pokwanitsa kugwira ntchito motsogoza zofuna a Malawi.

Mkamwa mwa Dr. Kabambe simutuluka mawu onyoza, kapena ovunda ayi, iwo amalemekeza kwambiri umunthu. Umenewu ndi umboni waukulu kuwonetsa kukhwima nzeru kwawo, komanso kusafuna kugawanitsa dziko kapena kugwetsera ena m’mavuto.

A Malawi sakusowekeranso chidziwitso ndi umboni wina kuposera kutiwonetsera a Kabambe monga amene chala cha ambuye chaloza kale. Ndipo nzika iloyonse yokonda dziko lake izindikire kuti Mulungu waloza kale Kabambe.

Tisayiwale kuti atsogoleli ena anabwera poyera kunena kuti “ukafuna kukhala wa chuma umayenera kukhala ka tambwali,” Dr. Kabambe sananenepo mawu ngati awa.

Dr. Kabambe akhala moyo wachipambano, wolimbika osati kuchita zinthu modziyalutsa ndi kusasamala umunthu. Zachinyengo, ndi zina zokayiyikitsa sadachite ndipo palibe chomwe chingatchinge tsogolo lawo pandale.

Ife a Malawi, ndikukudandaulirani kuti tisachite zinthu mobwelera m’mbuyo koma kupita chitsogolo, ngati tikufuna kusintha pachuma ndikupeza zomwe tikufuna ngati dziko, komanso kuwumba tsogolo labwino la ana athu, tisambwite koma kuvotera a Kabambe, ngati mtsogoleri wa nambala 7.

Tikaphonya kuvotera a Kabambe mkupatsa ena osadziwa za chuma, tidzalira tidzadziguguda pachifuwa mavuto atabalana khololophetge.

MAWU A DR BAKILI MULUZI
Dziko likumbukire mawu a Dr. Bakili Muluzi, omwe ananena kuti; nthawi yandale yapita, tachita ndale kokwanira pano pakufunika munthu wodziwa za chuma ndipo ndi Dr. Bingu Wa Mutharika”

LIWUMA LA DPP
Mawu ofunika ku DPP ngati muli okonda dziko lolani mgwirizano ndi zipani za UTM, PP, AFORD ndi zina kuti muwombole dzikoli.

Liwuma la DPP ndikusanva malangizo zidachititsa msanamira ndi mizati ina ya DPP kutulukamo mchipani kukayambitsa zipani zawo, monga Dr. Cassim Chilumpha, Dr. Joyce Banda, malemu Dr. Saulos Chilima, Dr. Kondwani Nankhumwa; onsewa ndi ana a DPP chifukwa chotseka mkutu ena akamayankhula.
DPP idziwe kuti ngati ikhale kotsutsa boma kuyambira pa 16 Sepitembala chaka chino, kutha kwachipani mkomweko basi

Lero: EVERYON CHIMULILENJI DZONZI msangalabwi za DPP kutulukamo mchipani chifukwa cha ndale zamtopola? Nanga awanso alakwanji? Kodi DPP idzamvanso?

DPP nthawi yochita chiganizo chanzeru ndi ino,osati kumadzalira chisankho chitadutsa muli kunja kwa boma. Khalani pansi ndi onse azipani zotsutsa boma mkupanga mgwirizano wamphamvu.

Oyenera kumusankha mkutsogolela, akuchita kudziwikiratu; a Malawi ali pakati posankha kupitilira kuvutika ndi umphawi, nkhanza, kusankhana mitundu, zigawo zochokera ndi kumasautsikabe ndi utsogoleri osautsa pansi pa Pulezidenti Lazarus Chakwera, kapena kusankha a Kabambe kuti atsogolele dziko kusintha kayendetsedwe ka chuma ndi kutukula miyoyo ya a Malawi.

ACHINYAMATA DZUKANI
Nthawi yakwana tsopano yofuna utsogoleri weniweni wadziko, utsogoleri wanzeru ndi wa masomphenya kuti akonze momwe atsogoleli ena kumbuyoku anasokoneza. A Malawi makamaka achinyamata tsogolo la dziko lino liri mmanja mwanu.

Chonde dzukani, chitani kanthu poteteza tsogolo lanu ndi voti yanu.

Wachinyamata wa nzeru akuyenera kuvotera Dr. Dalitso Kabambe, mnyamata nzawo komanso wanzeru zakuya.

Pa ichi achinyamata onse asapusitsidwe ndikuvotera chipani cha MCP ngati ena omwe ndi osakonda dziko angafune kuchitira. Omwe anazolowela kuchita ndale zachikale akhoza kutero, koma achinyamata sankhani a Kabambe .

Atsizinamtole omwe akulamula pano alibe ntchito ndi mavuto a Malawi, zawo zili bwino.

Atsogoleli otere amasamala zawo zokha ndikutaya tsogolo ladziko lino kudzenje mopanda chisoni.
Musalole atsogoleli ngati awa, ndipo chitani chotheka kukana izi ndi voti yanu.

Sibwino kungotsatira chigulu koma mukupita kuphompho ayi. Tikuyenela kupanga chiganizo chomanga dziko lathu, ngati sititero pano tidzawonelera dziko lino likuwonengeka kwa mnanu.

Dr. Dalitso Kabambe ndi mpulumutsi wadziko la Malawi, ndipo ndiye chiyembekezo chathu tonse.

Maravi Post Author

Today’s Opinion · Op-Ed Columnists · Editorials · Op-Ed Contributors to the Maravi Post· The Maravi Post accepts opinion essays on any topic. Published pieces typically run from 400 to 1,200 words, but drafts of any length within the bounds of reason will be considered.


Discover more from The Maravi Post

Subscribe to get the latest posts sent to your email.

Discover more from The Maravi Post

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading