Friday, June 14, 2024
HomeDevelopmentAMalawi 123, 000 apeza ntchito pamene Chakwera wakhazikitsa ntchito zomanga mafakitale

AMalawi 123, 000 apeza ntchito pamene Chakwera wakhazikitsa ntchito zomanga mafakitale

Watipaso Mzungu JNR

LILONGWE-(MaraviPost)-Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wati aMalawi okwana 123, 000 apeza ntchito makampani akayamba kumanga mafakitale awo kumalo omwe boma lawasankha mdziko lino.

Chakwera wanena izi Loweruka pamwambo wokhazikitsa ntchito yomanga mafakitate ku Lilongwe Industrial Park omwe akupezeka ku Magwero mumzinda wa Lilongwe.

Iwo anati kukhazikikitsa mafakitale ndi chimodzi mwa mfundo zomwe boma lawo layikapo mtima pofuna kutukula dziko lino.

“Mmasomphenya a Malawi 2063 omwe tonse aMalawi tinagwirizana kuti tiwakwaniritse muli msanamira zitatu zochurukitsira chuma cha dziko lathu, ndipo yoyamba ndi kumanga mafakitale. Mfundo imeneyi ikukamba ka kufunikila kwa ma fakitale opanga zinthu zosiyanasiyana mogwiritsa ntchito zokolola zomwe timapeza mminda yathu,” anafotokoza motere mtsogoleriyu.

Chakwera anadzudzula maulamuliro ammbuyomu kaamba kogulitsa makampani aboma ndi cholinga choti agawane ndalama.

Iwo anati kugulitsa makampani aboma ndi chomwe chidachititsa kuti mitengo ya katundu wambiri ikwere kaamba koti katundu wina aliyense yemwe aMalawi amagwiritsa ntchito anali wochokera kunja.

“Wina asakunamizeni. Zomwe zakhala zikuchitika mdziko muno, zomalola anthu andale ndi am’boma kuti azitenga ma fakitale ndi ma kampane a boma nkuwagulitsa mobetsa ndi zimene zabweretsa umphawi mdziko muno. Dziko lopanda ma fakitale ndi ma kampane ogwiritsa ntchito zokolola alimi mumakhala umphawi chifukwa alimi amasowa misika yogulitsira katundu wawo. Dziko lopanda ma fakitale ndi ma kampane ogwiritsa ntchito zokolola alimi mumakhala umphawi chifukwa katundu wa alimi amatulutsidwa ndi madobadoba amene saalabadira zoonjezera phindu pakatunduyo kuti alimi apeze ndalama yolozeka.

“Dziko lopanda ma fakitale ndi ma kampane ogwiritsa ntchito zokolola alimi mumakhala umphawi chifukwa anchinyamata saapeza ntchito. Dziko lopanda ma fakitale ndi ma kampane ogwiritsa ntchito zokolola alimi mumakhala umphawi chifukwa simupezeka forex yokwanira kuti amabizinesi azitha kugula zinthu zakunja, chifukwa chomwe chimabweretsa forex mdziko ndi katundu amene mafakitale ndi makampane anu amagulitsa mayiko akunja,” adatero tero Chakwera.

“Komanso mukamaona zinthu zikukwera mitengo modetsa nkhawa, wina asakunamizeni kuti zayamba lero kukwerako. Zinthu ku Malawi kuno zinayamba kukwera mtengo 1994 pamene tinkangoonelera andale akugulitsana ma kampane ndi mafakitale aboma. Dziko lopanda ma fakitale ndi ma kampane ogwiritsa ntchito zokolola alimi mitengo yazinthu amangoti yakwera yakweranso. Nchifukwa chani? Mitengo yazinthu siingasiye kukwera ngati mdziko mulibe makampane ndi ma fakitale opanga zinthu motchipa mMalawi mommuno kugwiritsa ntchito ma raw material amMalawi mommuno. Mitengo yazinthu siingasiye kukwera ngati mashopu athu mwadzadza zinthu zogula kunja, zinthu zomwe zimakhala zodhula kusiyana ndizopanga konkuno.

“Ndiye poti ma fakitale opanga zinthu konkuno tinawasiya andale ndi am’boma agulitse nkugawana ndalamazo, mapeto ake ndi amenewa, zinthu kumangokwera mtengo kuyambira 1994 mpaka lero. Ndiye wina akamanama kuti wakweza mitengo ya zinthu mdziko muno ndi Chakwera, ameneyotu achite manyazi, chifukwa ndinagulitsa makampane opanga shuga mMalawi muno kuti shuga azingokwera mtengo siine. Ameneyotu achite manyazi, chifukwa ndinagulitsa makampane opanga zovala kuti zovala zizingopezeka zakunja zomwe sizisiya kukwera mtengo siine. Ameneyotu achite manyazi, chifukwa ndinagulitsa Malawi Savings Bank kuti aMalawi azisowa banki yowapatsa ndalama yopangila bizinesi nkutsala ndi ma banki obwereketsa ndalama mwakatapila, zomwe zakhala zikukweza mitengo yazinthu siine. Ameneyotu achite manyazi, chifukwa ndinatseketsa mafakitale ogulitsa katundu kunja kuti mdziko muno muzikhala forex othandiza kuti ndalama ya kwacha isamangogwaigwa nkumakweza mitengo yazinthu siine,” anapitiriza motero.

Koma Chakwera anatsindika kuti iyeyo alibe nthawi yolimbana ndi anthu amene anabweretsa chisokonezo chimenechi mdziko muno, ponena kuti nthawi yomwe ali nayo iye ndiye ndi kubwezeretsa zinthu zomwe enawo anasakaza.

Maravi Post Author
Maravi Post Author
Today's Opinion · Op-Ed Columnists · Editorials · Op-Ed Contributors to the Maravi Post· The Maravi Post accepts opinion essays on any topic. Published pieces typically run from 400 to 1,200 words, but drafts of any length within the bounds of reason will be considered.
RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

- Advertisment -

Most Popular

Recent Comments

James Hastings Chidule on Malawi’ fistula recovery at 86%
WELLINGTON WITMAN MOSELIJAH LUNDUKA on The history of Ngoni Maseko in Malawi
Lisa Frank on Home
azw3 on Home
Define Regtech on Home
Tobias Kunkumbira on Malawi to roll out Typhoid vaccine
arena plus nba standings 2022 to 2023 ph on Home
David on Home
마산출장 on Home
Cristina Thomas on Home
Alicia Alvarado on Home
The History of online Casinos – Agora Poker – hao029 on The History of online Casinos
Five factors that will determine #NigeriaDecides2023 - NEWSCABAL on Leadership Is Difficult Because Governance Is Very Stubborn, By Owei Lakemfa
Asal Usul Texas Holdem Poker – Agora Poker – hao029 on The Origins of Texas Holdem Poker
Malawi has asked Mike Tyson to be its cannabis ambassador - Techio on Malawi lawmaker Chomanika against Mike Tyson’s appointment as Cannabis Brand Ambassador over sex offence
Finley Mbella on Brand Chakwera leaks Part 1
Maria Eduarda Bernardo on The 2021 Guide to Trading Forex Online
Atsogo Kemso, Political Foot Soldier on Why MCP and UTM Alliance Will Fail
Em. Prof. Willem Van Cotthem - Ghent University, Belgium on Malawi army, National bank cover Chilumba barrack with trees
Christopher Murdock on Why dating older woman is dangerous?
Samantha The Hammer on Why dating older woman is dangerous?